Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 15:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo munthu aliyense wakukhayo akamkhudza, osasambatu m'manja m'madzi, atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo munthu aliyense wakukhayo akamkhudza, osasambatu m'manja m'madzi, atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Aliyense amene munthu wotulutsa mafinyayo amkhudze asanasambe m'manja, achape zovala zake, ndipo asambe thupi lonse, koma akhalabe woipitsidwa mpaka madzulo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 “ ‘Munthu wotulutsa mafinyayo akakhudza munthu aliyense asanasambe mʼmanja, wokhudzidwayo achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 15:11
5 Mawu Ofanana  

Ndipo izi zikudetsani: aliyense akhudza mtembo wake adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo;


Ndipo munthu aliyense akakhudza kanthu kalikonse kadali pansi pake adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; ndipo iye wakunyamula zimenezo atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.


Ndipo zotengera zadothi wazikhudza wakukhayo, aziphwanye; ndi zamtengo, azitsuke ndi madzi.


Ndipo chilichonse munthu wodetsedwa achikhudza chidzakhala chodetsedwa; ndi munthu wakuchikhudza adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.


koma kudzali pofika madzulo, asambe m'madzi; ndipo litalowa dzuwa alowe pakati pa chigono.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa