Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 22:6 - Buku Lopatulika

6 munthu wokhudza chilichonse chotere adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo, ndipo asadye zinthu zopatulika, akapanda kusamba thupi lake ndi madzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 munthu wokhudza chilichonse chotere adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo, ndipo asadye zinthu zopatulika, akapanda kusamba thupi lake ndi madzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Wansembe aliyense wokhudza chinthu chotere, akhala woipitsidwa mpaka madzulo, ndipo asadyeko zinthu zopatulika mpaka atasamba thupi lonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Tsono ngati wansembe angakhudze chilichonse mwa zimenezi ndiye kuti adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Asadye chopereka chilichonse chopatulika mpaka atasamba thupi lake lonse.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 22:6
16 Mawu Ofanana  

Ndipo iliyonse iyenda yopanda chiboda mwa zamoyo zonse za miyendo inai, muiyese yodetsedwa; aliyense wokhudza mtembo wake adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.


Ndipo iye amene akanyamula mtembo wake atsuke zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; muziyese izi zodetsa.


Izi ndi zimene muziyese zodetsa, mwa zonse zakukwawa; aliyense azikhudza zitafa, adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.


Ndipo chilichonse chakufa cha izi chikagwera kanthu, kanthuka kadzakhala kodetsedwa; ngakhale chipangizo chamtengo, kapena chovala, kapena chikopa kapena thumba, chipangizo chilichonse chimene agwira nacho ntchito, achiviike m'madzi, ndipo chidzakhala chodetsedwa kufikira madzulo; pamenepo chidzakhala choyera.


Ndipo ikafa nyama yakudya, iye amene akhudza mtembo wake adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.


Ndipo iye wakudya kanthu ka mtembo wake azitsuka zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; iyenso wakunyamula mtembo wake atsuke zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.


Ndipo munthu aliyense wakukhudza kama wake azitsuka zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.


ndi aliyense wokhudza chinthu chokwawa chakudetsedwa nacho, kapenanso munthu amene akamdetsa nacho, chodetsa chake chilichonse;


Koma litalowa dzuwa, adzakhala woyera, ndi pambuyo pake adyeko zoyerazo, popeza ndizo chakudya chake.


Pamenepo Hagai anati, Munthu wodetsedwa ndi mtembo akakhudza kanthu ka izi, kodi kali kodetsedwa kanthuka? Ndipo ansembe anayankha nati, Kadzakhala kodetsedwa.


Ndipo chilichonse munthu wodetsedwa achikhudza chidzakhala chodetsedwa; ndi munthu wakuchikhudza adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.


Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m'dzina la Ambuye Yesu Khristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.


tiyandikire ndi mtima woona, m'chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbumtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa