Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 7:19 - Buku Lopatulika

19 Ndipo nyama yokhudza kanthu kalikonse kodetsa isadyeke; aitenthe ndi moto. Koma za nyama ina, aliyense ayera aidyeko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Ndipo nyama yokhudza kanthu kalikonse kodetsa isadyeke; aitenthe ndi moto. Koma za nyama ina, aliyense ayera aidyeko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 “Nyama imene ikhudza chinthu chilichonse chonyansa pa zachipembedzo, munthu asaidye, koma itenthedwe pa moto. Onse amene ali osaipitsidwa pa zachipembedzo angathe kudya nyama ya nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 “ ‘Nyama imene yakhudza chilichonse chodetsedwa, munthu asayidye, koma itenthedwe pa moto. Aliyense amene ali woyeretsedwa angathe kudya nyama inayo.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 7:19
12 Mawu Ofanana  

Aliyense akakhudza nyama yake adzakhala wopatulika; ndipo akawaza mwazi wake wina pa chovala chilichonse, utsuke chimene adauwazacho m'malo opatulika.


Ndipo akadyako nyama ya nsembe zoyamika zake tsiku lachitatu, sikuvomerezeka kumene; sadzamwerengera wobwera nayo; ndiyo chinthu chonyansa, ndipo munthu wakudyako adzasenza mphulupulu zake.


Koma munthu akadya nyama ya nsembe zoyamika za Yehova, pokhala nacho chomdetsa, munthuyo achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.


Koma patsani mphatso yachifundo za m'katimo; ndipo onani, zonse zili zoyera kwa inu.


ndipo anati kwa iwo, Mudziwa inu nokha kuti sikuloledwa kwa munthu Myuda adziphatike kapena kudza kwa munthu wa mtundu wina; koma Mulungu anandionetsera ine ndisanenere aliyense ali munthu wamba kapena wonyansa;


Ndidziwa, ndipo ndakhazikika mtima mwa Ambuye Yesu, kuti palibe chinthu chonyansa pa chokha; koma kwa ameneyo achiyesa chonyansa, kwa iye chikhala chonyansa.


Usapasule ntchito ya Mulungu chifukwa cha chakudya. Zinthu zonse zili zoyera; koma kuli koipa kwa munthu amene akudya ndi kukhumudwa.


Chifukwa chake, Tulukani pakati pao, ndipo patukani, ati Ambuye, Ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka; ndipo Ine ndidzalandira inu,


Zonse ziyera kwa iwo amene ayera mtima; koma kwa iwo odetsedwa ndi osakhulupirira kulibe kanthu koyera; komatu zadetsedwa nzeru zao ndi chikumbumtima chao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa