Pamenepo Hazaele mfumu ya Aramu anakwera, nathira nkhondo pa Gati, naulanda, nalunjikitsa nkhope yake kukwera ku Yerusalemu.
Numeri 18:9 - Buku Lopatulika Izi ndi zako pa zinthu zopatulika kwambiri, zosafika kumoto; zopereka zao zonse, ndi nsembe zao zonse zaufa, ndi nsembe zao zonse zauchimo, ndi nsembe zao zonse zopalamula, zimene andibwezera Ine, zikhale zopatulika kwambiri za iwe ndi za ana ako aamuna. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Izi ndi zako pa zinthu zopatulika kwambiri, zosafika kumoto; zopereka zao zonse, ndi nsembe zao zonse zaufa, ndi nsembe zao zonse zauchimo, ndi nsembe zao zonse zopalamula, zimene andibwezera Ine, zikhale zopatulika kwambiri za iwe ndi za ana ako amuna. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwa zopereka zoyera kopambana zimene sadazitenthe pa guwa, zanu zikhale izi: chepereka chonse cha chakudya, nsembe zao zonse zopepesera machimo ndi nsembe zao zonse zopepesera kupalamula, zimene amapereka kwa Ine, zonsezo zikhale zoyera kwa iwe ndi kwa ana ako. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Uzilandiranso gawo la zopereka zopatulika kwambiri zomwe sizinawotchedwe pa moto. Kuchokera pa mphatso zonse zimene amabweretsa kwa Ine ngati zopatulika kwambiri, nsembe zachakudya kapena nsembe zopepesera machimo, gawo limenelo ndi lako ndi ana ako aamuna. |
Pamenepo Hazaele mfumu ya Aramu anakwera, nathira nkhondo pa Gati, naulanda, nalunjikitsa nkhope yake kukwera ku Yerusalemu.
ndi ana athu oyamba kubadwa, ndi oyamba kubadwa a nyama zathu, monga mulembedwa m'chilamulo, ndi oyamba a ng'ombe zathu, ndi nkhosa zathu, kubwera nazo kunyumba ya Mulungu wathu kwa ansembe akutumikira m'nyumba ya Mulungu wathu;
Pamenepo anati kwa ine, Zipinda za kumpoto, ndi zipinda za kumwera, zili chakuno cha mpatawo, ndizo zipinda zopatulika, kumene ansembe okhala pafupi pa Yehova azidyera zinthu zopatulika kwambiri; kumeneko aziika zopatulika kwambiri, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula; pakuti malowo ndi opatulika.
Azidya nsembe yaufa, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula; ndipo zilizonse zoperekedwa chiperekere mu Israele ndi zao.
Mwalekeranji kudya nsembe yauchimo m'malo opatulika, pakuti ndiyo yopatulika kwambiri, ndipo Iye anakupatsani iyo, kuchotsera nayo mphulupulu ya khamulo, kuwachitira chowatetezera pamaso pa Yehova?
Ndipo akaphere mwanawankhosa wamwamuna paja amapherapo nsembe yauchimo, ndi nsembe yopsereza, pamalo opatulika; pakuti monga nsembe yauchimo momwemo nsembe yopalamula nja wansembe; ndiyo yopatulika kwambiri.
Ndipo chotsalira cha nsembe yaufa chikhale cha Aroni ndi ana ake; ndicho chopatulika kwambiri cha nsembe zamoto za Yehova.
Koma wansembe atakagula munthu ndi ndalama zake, iyeyu adyeko; ndi iwo amene anabadwa m'nyumba yake, adyeko mkate wake.
Koma litalowa dzuwa, adzakhala woyera, ndi pambuyo pake adyeko zoyerazo, popeza ndizo chakudya chake.
Akachimwa mkulu, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova Mulungu wake, napalamula;
Ndipo akachimwa wina wa anthu a m'dziko, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, napalamula;
Ndipo akachimwa munthu, wakuti adamva mau akuwalumbiritsa, ndiye mboni, kapena wakuona, kapena wakudziwa, koma osawulula, azisenza mphulupulu yake;
nadze nayo nsembe yopalamula kwa Yehova chifukwa cha kulakwa kwake adachimwira, ndiyo nkhosa yaikazi, kapena mbuzi yaikazi, ikhale nsembe yauchimo; ndipo wansembe amchitire chomtetezera chifukwa cha kuchimwa kwake.
Asachiphike ndi chotupitsa. Ndachipereka chikhale gawo lao lochokera pa nsembe zanga zamoto; ndicho chopatulika kwambiri, monga nsembe yauchimo, ndi monga nsembe yopalamula.
Koma asadye nsembe yauchimo iliyonse, imene amadza nao mwazi wake ku chihema chokomanako kutetezera nao m'malo opatulika; aitenthe ndi moto.
Monga nsembe yauchimo, momwemo nsembe yopalamula; pa zonse ziwirizi pali chilamulo chimodzi; ikhale yake ya wansembeyo, amene achita nayo chotetezera.
Ansembe Alevi, fuko lonse la Levi, alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi Israele; azizidya nsembe zamoto za Yehova, ndi cholowa chake.