Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 4:22 - Buku Lopatulika

22 Akachimwa mkulu, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova Mulungu wake, napalamula;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Akachimwa mkulu, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova Mulungu wake, napalamula;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 “Wolamula akachimwa mosadziŵa, kuchimwira Chauta, Mulungu wake, pa chinthu choletsedwa, napalamula pakutero,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 “ ‘Ngati mtsogoleri achimwa mosadziwa nachita zimene ndi zoletsedwa ndi Yehova Mulungu wake, ndiye kuti wapalamula.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 4:22
15 Mawu Ofanana  

Ndiponso muletse kapolo wanu pa zodzitama; zisachite ufumu pa ine. Pamenepo ndidzakhala wangwiro, ndi wosachimwa cholakwa chachikulu.


Koma iwe, dzisankhire mwa anthu ako onse, amuna anzeru, akuopa Mulungu, amuna oona, akudana nalo phindu la chinyengo; nuwaikire iwo oterewa, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, akulu a pa makumi;


Usalole m'kamwa mwako muchimwitse thupi lako; usanene pamaso pa mthenga kuti, Ndinaphophonya; Mulungu akwiyire mau ako chifukwa ninji, naononge ntchito ya manja ako?


Ndipo gulu lonse la Israele likalakwa osati dala, ndipo chikabisika chinthuchi pamaso pa msonkhano, litachita china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, ndi kupalamula;


Lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Munthu akachimwa, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, nakachitapo kanthu;


Ndipo akachimwa wina wa anthu a m'dziko, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, napalamula;


Ndipo munthu akachimwa, nakachita china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova; angakhale analibe kudziwa, koma wapalamula, azisenza mphulupulu yake.


Ndipo pamene mulakwa, osachita mau awa onse amene Yehova ananena ndi Mose;


pamenepo kudzali, ngati anachichita osati dala, osachidziwa khamulo, khamu lonse lipereke ng'ombe yamphongo ikhale nsembe yopsereza, ya fungo lokoma ya Yehova, pamodzi ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira, monga mwa chiweruzo chake; ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo.


ndipo anauka pamaso pa Mose, pamodzi ndi amuna mazana awiri mphambu makumi asanu a ana a Israele, ndiwo akalonga a khamulo, oitanidwa a msonkhano, amuna omveka.


Ndipo Mose, ndi Eleazara wansembe, ndi akalonga onse a khamulo, anatuluka kukomana nao kunja kwa chigono.


Pamenepo ana a Gadi ndi ana a Rubeni anadza nanena ndi Mose, ndi Eleazara wansembe, ndi akalonga a khamulo, nati,


muikire mizinda ikukhalireni mizinda yopulumukirako; kuti wakupha mnzake wosati dala athawireko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa