Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 10:36 - Buku Lopatulika

36 ndi ana athu oyamba kubadwa, ndi oyamba kubadwa a nyama zathu, monga mulembedwa m'chilamulo, ndi oyamba a ng'ombe zathu, ndi nkhosa zathu, kubwera nazo kunyumba ya Mulungu wathu kwa ansembe akutumikira m'nyumba ya Mulungu wathu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

36 ndi ana athu oyamba kubadwa, ndi oyamba kubadwa a nyama zathu, monga mulembedwa m'chilamulo, ndi oyamba a ng'ombe zathu, ndi nkhosa zathu, kubwera nazo kunyumba ya Mulungu wathu kwa ansembe akutumikira m'nyumba ya Mulungu wathu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

36 Tidzaperekanso kwa Mulungu ana athu aamuna oyamba kubadwa. Ana a ng'ombe oyamba kubadwa ndiponso ana oyamba kubadwa a nkhosa ndi a mbuzi zathu, tidzapereka kwa ansembe amene amatumikira ku Nyumba ya Mulungu, monga mudalembedwera m'Malamulo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

36 “Tidzabweranso nawo ku Nyumba ya Mulungu, kwa ansembe amene amatumikira ku Nyumba ya Mulungu ana athu aamuna oyamba kubadwa ndi ana angʼombe oyamba kubadwa monga zalembedwera mu Malamulo. Tidzaperekanso ana oyamba kubadwa a ziweto zathu ndi ana ankhosa oyamba kubadwa.”

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 10:36
14 Mawu Ofanana  

Ndipo pobuka mau aja, ana a Israele anapereka mochuluka, zobala zoyamba za tirigu, vinyo, ndi mafuta, ndi uchi, ndi za zipatso zonse za m'minda, ndi limodzi la magawo khumi la zonse anabwera nazo mochuluka.


Ndipo tsiku lomwelo anaika anthu asunge zipinda za chuma, za nsembe zokweza, za zipatso zoyamba, ndi za limodzilimodzi la magawo khumi, kulonga m'mwemo, monga mwa minda ya midzi, magawo onenedwa ndi chilamulo, akhale a ansembe ndi Alevi; popeza Yuda anakondwera nao ansembe ndi Alevi akuimirirako.


namkonzera chipinda chachikulu, kumene adasungira kale zopereka za ufa, lubani, ndi zipangizo, ndi limodzilimodzi la magawo khumi a tirigu, vinyo, ndi mafuta, zolamulidwira Alevi, ndi oimbira, ndi odikira, ndi nsembe zokweza za ansembe.


Ndipatulire Ine yense woyamba kubadwa, wotsegulira pa amake mwa ana a Israele, mwa anthu ndi mwa zoweta; ndiwo anga.


Uzibwera nazo zoyambayamba za m'munda mwako kunyumba ya Yehova Mulungu wako. Usaphike mwanawambuzi mu mkaka wa make.


Onse oyambira kubadwa ndi anga; ndi zoweta zanu zonse zazimuna, zoyamba za ng'ombe ndi za nkhosa.


Mubwere nalo limodzilimodzi lonse la khumi, kunyumba yosungiramo, kuti m'nyumba mwanga mukhale chakudya; ndipo mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.


Pakuti ana oyamba onse ndi anga; tsiku lija ndinakantha ana oyamba onse m'dziko la Ejipito ndinadzipatulira ana oyamba onse mu Israele, kuyambira munthu kufikira choweta; ndiwo anga; Ine ndine Yehova.


Koma iye amene aphunzira mau, ayenera kuchereza womphunzitsayo m'zonse zabwino.


ndi kubwera nazo kumeneko nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zophera, ndi magawo anu onse a magawo khumi, ndi nsembe yokweza ya dzanja lanu, ndi zowinda zanu, ndi nsembe zanu zaufulu, ndi zoyamba kubadwa za ng'ombe zanu, ndi za nkhosa ndi mbuzi zanu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa