Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Nehemiya 10:35 - Buku Lopatulika

35 ndi kubwera nazo zipatso zoyamba za nthaka, ndi zoyamba za zipatso zonse za mtengo uliwonse chaka ndi chaka, ku nyumba ya Yehova;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

35 ndi kubwera nazo zipatso zoyamba za nthaka, ndi zoyamba za zipatso zonse za mtengo uliwonse chaka ndi chaka, ku nyumba ya Yehova;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

35 Tikulonjezanso kuti tidzabwera ndi zipatso zoyamba kucha za kuminda kwathu, ndi zipatso zoyamba kucha za mtengo uliwonse wazipatso, chaka ndi chaka, kuti tizipereke ku Nyumba ya Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

35 “Tilonjezanso kuti tidzabwera ndi zipatso zoyamba kucha za mʼminda yathu ndi zipatso zoyamba kucha za mtengo uliwonse wa zipatso chaka ndi chaka kuti tidzapereke ku Nyumba ya Mulungu wathu.”

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 10:35
13 Mawu Ofanana  

ndi chopereka cha nkhuni pa nthawi zoikika, ndi wa zipatso zoyamba. Mundikumbukire, Mulungu wanga, chindikomere.


Uzibwera nazo zoyambayamba za m'munda mwako kunyumba ya Yehova Mulungu wako. Usaphike mwanawambuzi mu mkaka wa make.


Uzibwera nazo zipatso zoyambayamba za nthaka yako kunyumba ya Yehova Mulungu wako. Usaphika mwanawambuzi mu mkaka wa make.


Ndi zoyamba za zipatso zoyamba za zinthu zilizonse, ndi nsembe zokweza zilizonse za nsembe zanu zonse zokweza nza ansembe; muperekenso ufa wanu woyamba kwa wansembe, kuti mdalitso ukhalebe pa nyumba yako.


kapena chilichonse analumbirapo monama; achibwezere chonsechi, naonjezepo, limodzi la magawo asanu; apereke ichi kwa mwini wake tsiku lotsutsidwa iye.


Ndipo adze nayo nsembe yake yopalamula kwa Yehova, ndiyo nkhosa yamphongo yopanda chilema ya m'khola mwake, monga umayesa mtengo wake, ikhale nsembe yopalamula, adze nayo kwa wansembe;


Mafuta onse okometsetsa, ndi vinyo watsopano, ndi tirigu yense wokometsetsa. Zipatso zao zoyamba zimene aziperekako kwa Yehova, ndazipereka kwa iwe.


Ndiponso abale ako, fuko la Alevi, fuko la kholo lako, uwayandikizitse pamodzi ndi iwe, kuti aphatikane ndi iwe, ndi kukutumikira; koma iwe ndi ana ako pamodzi ndi iwe mukhale ku khomo la chihema cha mboni.


kuti muzitengako zoyamba za zipatso zonse za nthaka, zakubwera nazo inu zochokera m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani; ndi kuziika mudengu, ndi kupita ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa