Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Nehemiya 10:37 - Buku Lopatulika

37 ndi kuti tidzabwera nazo za mtanda wa mkate wathu woyamba, ndi nsembe zathu zokwera, ndi zipatso za mtengo uliwonse, vinyo, ndi mafuta, kwa ansembe, kuzipinda za nyumba ya Mulungu wathu; ndi limodzi la magawo khumi la nthaka yathu kwa Alevi; pakuti Alevi amene amalandira limodzilimodzi la magawo khumi m'midzi yonse yolima ife.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

37 ndi kuti tidzabwera nazo za mtanda wa mkate wathu woyamba, ndi nsembe zathu zokwera, ndi zipatso za mtengo uliwonse, vinyo, ndi mafuta, kwa ansembe, kuzipinda za nyumba ya Mulungu wathu; ndi limodzi la magawo khumi la nthaka yathu kwa Alevi; pakuti Alevi amene amalandira limodzilimodzi la magawo khumi m'midzi yonse yolima ife.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

37 Ndipo ku zipinda za Nyumba ya Mulungu wathu, tidzaperekanso kwa ansembewo mtanda wathu wa buledi wa ufa woyamba, ndiponso mphatso zathu zina, monga zipatso za mtengo uliwonse, vinyo ndi mafuta. Tidzaperekanso kwa Alevi chimodzi mwa zigawo khumi za zinthu za m'minda mwathu, pakuti Alevi ndiwo amene amasonkhanitsa zigawo zonse zachikhumi m'midzi yathu yonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

37 “Ndiponso ku zipinda za Nyumba ya Mulungu wathu, kwa ansembe tidzaperekanso mtanda wathu wa buledi wa ufa ndi mphatso zina monga zipatso za mtengo uliwonse, vinyo ndi mafuta. Tidzaperekanso kwa alevi chakhumi cha mbewu zathu pakuti alevi ndiwo amasonkhanitsa chakhumi mʼmidzi yathu yonse.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 10:37
23 Mawu Ofanana  

Ndi ana a Israele ndi Yuda okhala m'mizinda ya Yuda, iwonso anabwera nalo limodzi la magawo khumi la ng'ombe, ndi nkhosa, ndi limodzi la magawo khumi la zinthu zopatulika, zopatulikira Yehova Mulungu wao; naziunjika miyulumiyulu.


Ndinazindikiranso kuti sanapereke kwa Alevi magawo ao; m'mwemo Alevi ndi oimbira adathawira yense kumunda wake.


Ndi Ayuda onse anabwera nalo limodzilimodzi la magawo khumi a tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, kunyumba za chuma.


namkonzera chipinda chachikulu, kumene adasungira kale zopereka za ufa, lubani, ndi zipangizo, ndi limodzilimodzi la magawo khumi a tirigu, vinyo, ndi mafuta, zolamulidwira Alevi, ndi oimbira, ndi odikira, ndi nsembe zokweza za ansembe.


Pamenepo ndinalamulira, ndipo anayeretsa zipindazo; ndipo ndinabwezeramonso zipangizo za nyumba ya Mulungu, pamodzi ndi zopereka za ufa ndi lubani.


kuti uzikapatulira Yehova onse oyamba kubadwa ndi oyamba onse uli nao odzera kwa zoweta; amunawo ndi a Yehova.


Ndipatulire Ine yense woyamba kubadwa, wotsegulira pa amake mwa ana a Israele, mwa anthu ndi mwa zoweta; ndiwo anga.


Mutuluke nayo m'zinyumba zanu mikate iwiri ya nsembe yoweyula, ikhale ya awiri a magawo khumi a efa; ikhale ya ufa wosalala, yopanga ndi chotupitsa, zipatso zoyamba za Yehova.


Mubwere nalo limodzilimodzi lonse la khumi, kunyumba yosungiramo, kuti m'nyumba mwanga mukhale chakudya; ndipo mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.


Kodi munthu adzalanda za Mulungu? Ndipo inu mundilanda Ine. Koma mukuti, Takulandani zotani? Limodzilimodzi la magawo khumi, ndi zopereka.


Zilizonse zoyambira kubadwa mwa zamoyo zonse zimene abwera nazo kwa Yehova, mwa anthu ndi mwa nyama, ndi zako; koma munthu woyamba kubadwa uzimuombola ndithu; ndi nyama yodetsa yoyamba kubadwa uziiombola.


Ndipo nyama yake ndi yako, ndiyo nganga ya nsembe yoweyula ndi mwendo wathako wa kulamanja, ndizo zako.


Ndipo taonani, ndawaninkha ana a Levi limodzi la magawo khumi mwa zonse mu Israele, likhale cholowa chao, mphotho ya pa ntchito yao alikuichita, ntchito ya chihema chokomanako.


Ndipo ngati zipatso zoyamba zili zopatulika, choteronso mtanda; ndipo ngati muzu uli wopatulika, choteronso nthambi.


Muzipereka ndithu limodzi la magawo khumi la zipatso zonse za mbeu zanu, zofuma kumunda, chaka ndi chaka.


Zipatso zoyamba za tirigu wanu, za vinyo wanu, ndi za mafuta anu ndi ubweya woyamba kuusenga, muwapatse izi.


kuti muzitengako zoyamba za zipatso zonse za nthaka, zakubwera nazo inu zochokera m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani; ndi kuziika mudengu, ndi kupita ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa