Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 7:6 - Buku Lopatulika

6 Amuna onse a mwa ansembe adyeko; adyere m'malo opatulika; ndiyo yopatulika kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Amuna onse a mwa ansembe adyeko; adyere m'malo opatulika; ndiyo yopatulika kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Munthu wamwamuna aliyense wa m'banja la ansembe angathe kudyako. Aidyere pa malo oyera. Imeneyo ndiyo nsembe yoyera kopambana.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Munthu wamwamuna aliyense wa mʼbanja la wansembe angathe kudyako nsembeyo koma adyere ku malo opatulika. Imeneyi ndi nsembe yopatulika kwambiri.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 7:6
11 Mawu Ofanana  

Pamenepo anati kwa ine, Zipinda za kumpoto, ndi zipinda za kumwera, zili chakuno cha mpatawo, ndizo zipinda zopatulika, kumene ansembe okhala pafupi pa Yehova azidyera zinthu zopatulika kwambiri; kumeneko aziika zopatulika kwambiri, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula; pakuti malowo ndi opatulika.


Ndipo chotsalira cha nsembe yaufa chikhale cha Aroni ndi ana ake; ndicho chopatulika kwambiri cha nsembe zamoto za Yehova.


Adye chakudya cha Mulungu wake, chopatulika kwambiri, ndi chopatulika;


Pamenepo avule zovala zake, navale zovala zina, nachotse phulusa kunka nalo kunja kwa chigono, kumalo koyera.


Amuna onse a mwa ansembe adyeko; ndiyo yopatulika kwambiri.


ndipo wansembe atenthe izi paguwa la nsembe, nsembe yamoto ya kwa Yehova; ndiyo nsembe yopalamula.


Munthu akanyamulira nyama yopatulika m'ngudulira, nakhudza mkate, kapena ndiwo, kapena vinyo, kapena mafuta, kapena chakudya chilichonse, ndi ngudulira, kodi chisandulika chopatulika? Ndipo ansembe anayankha nati, Iai.


Tapenyani Israele monga mwa thupi; kodi iwo akudya nsembezo alibe chiyanjano ndi guwa la nsembe?


Kodi simudziwa kuti iwo akutumikira za Kachisi amadya za mu Kachisi, ndi iwo akuimirira guwa la nsembe, agawana nalo guwa la nsembe?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa