Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 4:27 - Buku Lopatulika

27 Ndipo akachimwa wina wa anthu a m'dziko, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, napalamula;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Ndipo akachimwa wina wa anthu a m'dziko, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, napalamula;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 “Ngati munthu wamba aliyense achimwa mosadziŵa, pochita china chilichonse chimene Chauta amaletsa, napalamula pakutero,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 “ ‘Ngati munthu wamba achimwa mosadziwa nachita zimene ndi zoletsedwa ndi Yehova, ndiye kuti wapalamula.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 4:27
14 Mawu Ofanana  

Ndiponso muletse kapolo wanu pa zodzitama; zisachite ufumu pa ine. Pamenepo ndidzakhala wangwiro, ndi wosachimwa cholakwa chachikulu.


Pakhale lamulo lomweli pa wobadwa m'dziko, ndi pa mlendo wakukhala pakati pa inu.


Ndipo udindo wa kalonga ndiwo kupereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi nsembe zothira, pachikondwerero, ndi pokhala mwezi, ndi pa masabata; pa zikondwerero zonse zoikika a nyumba ya Israele; ndipo apereke nsembe yauchimo, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yopsereza, ndi nsembe zamtendere, kuchitira chotetezera nyumba ya Israele.


Tsiku lachisanu ndi chiwiri la mweziwo uchitire momwemo aliyense wolakwa ndi wopusa; motero muchitire Kachisiyo chomtetezera.


Ndipo gulu lonse la Israele likalakwa osati dala, ndipo chikabisika chinthuchi pamaso pa msonkhano, litachita china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, ndi kupalamula;


Lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Munthu akachimwa, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, nakachitapo kanthu;


Akachimwa mkulu, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova Mulungu wake, napalamula;


Ndipo munthu akachimwa, nakachita china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova; angakhale analibe kudziwa, koma wapalamula, azisenza mphulupulu yake.


Ndipo anabwera nacho chopereka cha anthu, natenga mbuzi ya nsembe yauchimo ndiyo ya kwa anthu, naipha, naipereka nsembe yauchimo, monga yoyamba ija.


Pakhale chilamulo chimodzi ndi chiweruzo chimodzi kwa inu ndi kwa mlendo wakukhala kwanu.


Ndipo pamene mulakwa, osachita mau awa onse amene Yehova ananena ndi Mose;


Ndipo akachimwa munthu mmodzi osati dala, abwere nayo mbuzi yaikazi ya chaka chimodzi, ikhale nsembe yauchimo.


Kunena za wobadwa m'dziko mwa ana a Israele, ndi mlendo wakukhala pakati pao, mukhale nacho chilamulo chimodzi kwa iye wakuchita kanthu kosati dala.


Nena ndi ana a Israele, ndi kuti Mwamuna kapena mkazi akachita tchimo lililonse amachita anthu, kuchita mosakhulupirika pa Yehova, nakapalamuladi;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa