Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 7:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo chilamulo cha nsembe yopalamula ndi ichi: ndiyo yopatulika kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo chilamulo cha nsembe yopalamula ndi ichi: ndiyo yopatulika kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 “Nsembe yopepesera kupalamula njoyera kopambana. Lamulo lake ndi ili:

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 “ ‘Malamulo a nsembe yopepesera kupalamula imene ndi nsembe yopatulika kwambiri ndi awa:

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 7:1
17 Mawu Ofanana  

Ndipo Kore mwana wa Imina Mlevi, wa kuchipata cha kum'mawa, anayang'anira zopereka zaufulu za Mulungu, kugawira nsembe zokweza za Yehova, ndi zopatulika kwambiri.


Ndipo m'khonde la pachipata munali magome awiri chakuno, ndi magome awiri chauko, kuti apherepo nsembe yopsereza, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula.


Azidya nsembe yaufa, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula; ndipo zilizonse zoperekedwa chiperekere mu Israele ndi zao.


Ndipo anati kwa ine, Pano ndipo ansembe aziphikira nsembe yopalamula, ndi nsembe yauchimo; kumenenso aziotcha mikate ya ufa wa nsembe, kuti asatuluke nazo kubwalo lakunja ndi kupatulikitsa anthu.


Adye chakudya cha Mulungu wake, chopatulika kwambiri, ndi chopatulika;


Koma chuma chake chikapanda kufikira njiwa ziwiri kapena maunda awiri, wochimwayo azidza nacho chopereka chake limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, likhale la nsembe yauchimo; asamaikapo mafuta, kapena kuikapo lubani ai; pakuti ndicho nsembe yauchimo.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,


Munthu akachita mosakhulupirika, nakachimwa osati dala, pa zopatulika za Yehova, azidza nayo nsembe yake yopalamula kwa Yehova, ndiyo nkhosa yamphongo yopanda chilema, ya m'gulu lake, monga umayesa mtengo wake potchula masekeli a siliva, kunena sekeli wa malo opatulika, ikhale nsembe yopalamula;


Ndipo chuma chake chikapanda kufikira nkhosa, wochimwayo adze nayo kwa Yehova nsembe yake yopalamula, njiwa ziwiri, kapena maunda awiri; imodzi ikhale ya nsembe yauchimo, ndi ina ya nsembe yopsereza.


Ndipo adze nazo kwa wansembe, ndiye ayambe kubwera nayo ija ya kwa nsembe yauchimo, napotole mutu wake pakhosi pake, osauchotsa;


Asachiphike ndi chotupitsa. Ndachipereka chikhale gawo lao lochokera pa nsembe zanga zamoto; ndicho chopatulika kwambiri, monga nsembe yauchimo, ndi monga nsembe yopalamula.


Lankhula ndi Aroni ndi ana ake, ndi kuti, Chilamulo cha nsembe yauchimo ndi ichi: Pamalo pophera nsembe yopsereza ndipo pophera nsembe yauchimo pamaso pa Yehova; ndiyo yopatulika kwambiri.


Ndipo awapatulire Yehova masiku a kusala kwake, nadze nayo nkhosa yamphongo ya chaka chimodzi ikhale nsembe yopalamula; koma masiku adapitawa azikhala chabe, popeza anadetsa kusala kwake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa