Numeri 16:15 - Buku Lopatulika Pamenepo Mose adapsa mtima, ndipo anati kwa Yehova, Musasamalira chopereka chao; sindinalande bulu wao mmodzi, kapena kuchitira choipa mmodzi wa iwowa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Mose adapsa mtima, ndipo anati kwa Yehova, Musasamalira chopereka chao; sindinalanda bulu wao mmodzi, kapena kuchitira choipa mmodzi wa iwowa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Mose adapsa mtima kwambiri, ndipo adauza Chauta kuti, “Musalandire nsembe za anthu ameneŵa. Sindidaŵalande ndi bulu mmodzi yemwe, ndipo sindidalakwire ndi mmodzi yemwe mwa iwo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo Mose anakwiya kwambiri ndipo anati kwa Yehova, “Musalandire chopereka chawo. Sindinatenge kalikonse kwa iwo ngakhale bulu, ndiponso sindinalakwire wina aliyense wa iwo.” |
Ndipo kunali, pamene anayandikiza chigono, anaona mwanawang'ombeyo ndi kuvinako; ndipo Mose anapsa mtima, nataya magome ali m'manja mwake, nawaswa m'tsinde mwa phiri.
Ndipo Mose anati kwa Kora, Iwe ndi khamu lako lonse mukhale pamaso pa Yehova mawa, iwe ndi iwowa, ndi Aroni;
koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe: adzakhala wopalamula Gehena wamoto.
Ndipo m'mene anawaunguza ndi mkwiyo, ndi kumva chisoni chifukwa cha kuuma kwa mitima yao, ananena kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo analitambasula; ndipo linachira dzanja lake.
Koma ine sindinachite nako kanthu ka izi; ndipo sindilemba izi kuti chikakhale chotero ndi ine; pakuti kundikomera ine kufa, koma wina asayese kwachabe kudzitamanda kwanga.
Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbumtima chathu, kuti m'chiyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'chisomo cha Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu.
Tipatseni malo; sitinamchitire munthu chosalungama, sitinaipse munthu, sitinachenjerere munthu.
Inu ndinu mboni, Mulungunso, kuti tinakhala oyera mtima ndi olungama ndi osalakwa kwa inu akukhulupirira;