Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 7:2 - Buku Lopatulika

2 Tipatseni malo; sitinamchitire munthu chosalungama, sitinaipse munthu, sitinachenjerere munthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Tipatseni malo; sitinamchitira munthu chosalungama, sitinaipsa munthu, sitinachenjerera munthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Mutipatse malo m'mitima mwanu. Sitidalakwire munthu aliyense, kapena kumuipitsa, kapena kumchenjerera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mutipatse malo mʼmitima mwanu. Ife sitinalakwire munthu aliyense, kapena kuyipitsa munthu aliyense, kapena kumuchenjerera munthu aliyense.

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 7:2
23 Mawu Ofanana  

Pamenepo Mose adapsa mtima, ndipo anati kwa Yehova, Musasamalira chopereka chao; sindinalande bulu wao mmodzi, kapena kuchitira choipa mmodzi wa iwowa.


Ndipo yemwe sadzakulandirani inu kapena kusamva mau anu, pamene mulikutuluka m'nyumbayo, kapena m'mudzimo, sansani fumbi m'mapazi anu.


Iye wakulandira inu, andilandira Ine, ndi wakundilandira Ine, amlandira Iye amene ananditumiza Ine.


Ndipo m'mudzi uliwonse mukalowamo, ndipo alandira inu, idyani zomwezi akupatsani;


Sindinasirira siliva, kapena golide, kapena chovala cha munthu aliyense.


Pakuti otere satumikira Ambuye wathu Khristu, koma mimba yao; ndipo ndi mau osalaza ndi osyasyalika asocheretsa mitima ya osalakwa.


Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbumtima chathu, kuti m'chiyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'chisomo cha Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu.


Ndinenanso, Munthu asandiyese wopanda nzeru; koma ngati mutero, mundilandirenso ine monga wopanda nzeru, kuti inenso ndidzitamandire pang'ono.


ndipo pakukhala nanu, ndi kusowa, sindinasaukitse munthu aliyense; pakuti abale akuchokera ku Masedoniya, anakwaniritsa kusowa kwanga; ndipo m'zonse ndinachenjera ndekha, ndisalemetse inu, ndipo ndidzachenjerapo.


koma takaniza zobisika za manyazi, osayendayenda mochenjerera, kapena kuchita nao mau a Mulungu konyenga; koma ndi maonekedwe a choonadi; tidzivomeretsa tokha ku chikumbumtima cha anthu onse pamaso pa Mulungu.


Chifukwa chake mumlandire mwa Ambuye, ndi chimwemwe chonse; nimuchitire ulemu oterewa;


Aristariko wam'ndende mnzanga akupatsani moni, ndi Marko, msuweni wa Barnabasi (amene munalandira zolamulira za kwa iye; akafika kwanu, mumlandire iye),


Inu ndinu mboni, Mulungunso, kuti tinakhala oyera mtima ndi olungama ndi osalakwa kwa inu akukhulupirira;


amene ndi yemweyo ndakubwezera iwe, ndiye mtima weniweni wa ine.


Ngati tsono undiyesa woyanjana nawe, umlandire iye monga ine mwini.


Munthu akadza kwa inu, wosatenga chiphunzitso ichi, musamlandire iye kunyumba, ndipo musampatse moni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa