Numeri 12:3 - Buku Lopatulika Koma munthuyu Mose ndiye wofatsa woposa anthu onse a padziko lapansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma munthuyu Mose ndiye wofatsa woposa anthu onse a pa dziko lapansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Mose anali munthu wofatsa kupambana anthu onse a pa dziko lapansi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (Koma Mose anali munthu wodzichepetsa kwambiri kuposa munthu aliyense pa dziko lapansi). |
Ndipo Yehova anati kwa Mose, ndi Aroni, ndi Miriyamu modzidzimutsa, Tulukani inu atatu kudza ku chihema chokomanako. Pamenepo anatuluka atatuwo.
Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.
Tauzani mwana wamkazi wa Ziyoni, Taona, mfumu yako idza kwa iwe, wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi pa kabulu, mwana wa nyama yonyamula katundu.
Koma ine ndekha Paulo, ndidandaulira inu mwa kufatsa ndi ulere wa Khristu, ine amene pamaso panu ndikhala wodzichepetsa pakati pa inu, koma pokhala kwina ine ndilimbika mtima kwa inu;
Ndakhala wopanda nzeru, mwandichititsa kutero; pakuti inu munayenera kundivomereza; pakuti sindiperewere ndi atumwi oposatu m'kanthu konse, ndingakhale ndili chabe.
Ndani ali wanzeru, ndi waluso mwa inu? Aonetsere ndi mayendedwe ake abwino ntchito zake mu nzeru yofatsa.
koma kukhale munthu wobisika wamtima, m'chovala chosaola cha mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu.