Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 21:5 - Buku Lopatulika

5 Tauzani mwana wamkazi wa Ziyoni, Taona, mfumu yako idza kwa iwe, wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi pa kabulu, mwana wa nyama yonyamula katundu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Tauzani mwana wamkazi wa Ziyoni, Taona, mfumu yako idza kwa iwe, wofatsa ndi wokwera pa bulu, ndi pa kabulu, mwana wa nyama yonyamula katundu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 “Uzani mzinda wa Ziyoni kuti, ‘Ona mfumu yako ikudza kwa iwe. Ndi yodzichepetsa ndipo yakwera pa bulu. Zoonadi yakwera pa kabulu, mwana wa nyama yosenza katundu.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 “Uza mwana wamkazi wa Ziyoni, taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe, yofatsa ndi yokwera pa bulu, pa kamwana ka bulu, mwana wa nyama yonyamula katundu.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 21:5
39 Mawu Ofanana  

Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye.


Ndipo mfumu inanena ndi Ziba, Ulikutani ndi zimenezi? Nati Ziba, Abuluwo ndiwo kuti akaberekepo a pa banja lanu; ndi mitanda ya mikate ndi zipatso za m'dzinja ndizo zakudya za anyamata; ndi vinyoyo akufooka m'chipululu akamweko.


Ndipo mfumu inati kwa iwo, Tengani akapolo a mfumu yanu, nimukweze Solomoni mwana wanga pa nyuru yangayanga, nimutsikire naye ku Gihoni.


Ndipo Solomoni anasonkhanitsa magaleta ndi apakavalo; anali nao magaleta chikwi chimodzi mphambu mazana anai, ndi apakavalo zikwi khumi mphambu ziwiri, nawasungira m'mizinda yosungamo magaleta, ndi kwa mfumu mu Yerusalemu.


Kuti ndibukitse lemekezo lanu lonse; pa bwalo la mwana wamkazi wa Ziyoni, ndidzakondwera nacho chipulumutso chanu.


Tafuula, takuwa iwe, wokhala mu Ziyoni, chifukwa Woyera wa Israele wa m'kati mwako ali wamkulu.


Iwe amene utengera mau abwino ku Ziyoni, kwera iwe pamwamba paphiri lalitali; iwe amene utengera mau abwino ku Yerusalemu, kweza mau ako ndi mphamvu, kwezetsa usaope, nena kumizinda ya Yuda, Taonani, Mulungu wanu!


Taonani, Yehova walalikira kufikira malekezero a dziko lapansi. Nenani kwa mwana wamkazi wa Ziyoni, Taona chipulumutso chako chifika; taona mphotho yake ali nayo, ndi ntchito yake ili pamaso pake.


Ndipo Ine Yehova ndidzakhala Mulungu wao, ndi mtumiki wanga Davide kalonga pakati pao; Ine Yehova ndanena.


Ndi mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu yao, ndipo iwo onse adzakhala ndi mbusa mmodzi, adzayendanso m'maweruzo anga, nadzasunga malemba anga ndi kuwachita.


Koma ndidzachitira chifundo nyumba ya Yuda, ndi kuwapulumutsa mwa Ine Yehova Mulungu wao, osawapulumutsa ndi uta, kapena lupanga, kapena nkhondo ndi akavalo, kapena apakavalo.


Koma iwe, Betelehemu Efurata, ndiwe wamng'ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditulukira wina wakudzakhala woweruza mu Israele; matulukiro ake ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.


Ndipo wina wotuluka mu Yakobo adzachita ufumu; nadzapasula otsalira m'mizinda.


Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.


nati, Ali kuti amene anabadwa mfumu ya Ayuda? Chifukwa tinaona nyenyezi yake kum'mawa, ndipo tinadzera kudzamlambira Iye.


Ndipo iwe Betelehemu, dziko la Yudeya, sukhala konse wamng'onong'ono mwa akulu a Yudeya. Pakuti Wotsogolera adzachokera mwa iwe, amene adzaweta anthu anga Aisraele.


Ndipo ophunzirawo anamuka, nachita monga Yesu anawauza;


Ndipo anayamba kwa Mose, ndi kwa aneneri onse nawatanthauzira iwo m'malembo onse zinthu za Iye yekha.


Natanaele anayankha Iye, Rabi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu, ndinu mfumu ya Israele.


Koma ine ndekha Paulo, ndidandaulira inu mwa kufatsa ndi ulere wa Khristu, ine amene pamaso panu ndikhala wodzichepetsa pakati pa inu, koma pokhala kwina ine ndilimbika mtima kwa inu;


Koma asadzichulukitsire akavalo iye, kapena kubwereretsa anthu anke ku Ejipito, kuti achulukitse akavalo; popeza Yehova anati nanu, Musamabwereranso njira iyi.


Ndipo anali nao ana aamuna makumi anai ndi zidzukulu zazimuna makumi atatu, akuyenda okwera pa ana a abulu makumi asanu ndi awiri; naweruza Israele zaka zisanu ndi zitatu.


Inu akuyenda okwera pa abulu oyera, inu akukhala poweruzira, ndi inu akuyenda m'njira, fotokozerani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa