Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 12:11 - Buku Lopatulika

11 Ndakhala wopanda nzeru, mwandichititsa kutero; pakuti inu munayenera kundivomereza; pakuti sindiperewere ndi atumwi oposatu m'kanthu konse, ndingakhale ndili chabe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndakhala wopanda nzeru, mwandichititsa kutero; pakuti inu munayenera kundivomereza; pakuti sindiperewera ndi atumwi oposatu m'kanthu konse, ndingakhale ndili chabe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Ndasanduka wopusa, koma ndinu mwandichititsa zimenezi. Ndinu mukadayenera kundichitira umboni. Pakuti ngakhale sindili kanthu, atumwi anu apamwamba aja sandipambana pa kanthu kalikonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Ndadzisandutsa wopusa, koma inu mwandichititsa zimenezi. Ndinu amene munayenera kundichitira umboni. Ngakhale kuti sindine kanthu, koma sindine wochepetsetsa kwa “atumwi apamwamba” aja.

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 12:11
17 Mawu Ofanana  

Wina akutume, si m'kamwa mwako ai; mlendo, si milomo ya iwe wekha.


Chotero inunso m'mene mutachita zonse anakulamulirani, nenani, Ife ndife akapolo opanda pake, tangochita zimene tayenera kuzichita.


Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndili nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndilibe chikondi, ndili chabe.


ngati Paulo, kapena Apolo, kapena Kefa, kapena dziko lapansi, kapena moyo, kapena imfa, kapena za makono ano, kapena zilinkudza; zonse ndi zanu;


Koma ngati tisautsidwa, kuli chifukwa cha chitonthozo ndi chipulumutso chanu; ngati titonthozedwa, kuli kwa chitonthozo chanu chimene chichititsa mwa kupirira kwa masautso omwewo amene ifenso timva.


Bwenzi mutandilola pang'ono ndi chopusacho! Komanso mundilole.


Pakuti ndiyesa kuti sindinaperewere konse ndi atumwi oposatu.


Zizindikirotu za mtumwi zinachitika pakati pa inu, m'chipiriro chonse, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi zamphamvu.


Pakuti ngati ndikafuna kudzitamandira, sindidzakhala wopanda nzeru; pakuti ndidzanena choonadi; koma ndileka, kuti wina angandiwerengere ine koposa kumene andiona ine, kapena amva za ine.


Kodi tilikuyambanso kudzivomereza tokha? Kapena kodi tisowa, monga ena, makalata otivomerezetsa kwa inu, kapena ochokera kwa inu?


Pakuti ngati tili oyaluka, titero kwa Mulungu; ngati tili a nzeru zathu, titero kwa inu.


Pakuti ngati wina ayesa ali kanthu pokhala ali chabe, adzinyenga yekha.


Kwa ine wochepa ndi wochepetsa wa onse oyera mtima anandipatsa chisomo ichi ndilalikire kwa amitundu chuma chosalondoleka cha Khristu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa