ndipo ndidzakulumbiritsa iwe pa Yehova, Mulungu wa Kumwamba, ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti usadzamtengere mwana wanga mkazi wa kwa ana aakazi a Akananiwo, amene ndikhala pakati pao.
Numeri 12:1 - Buku Lopatulika Ndipo Miriyamu ndi Aroni anatsutsana naye Mose chifukwa cha mkazi mtundu wake Mkusi amene adamtenga; popeza adatenga mkazi Mkusi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Miriyamu ndi Aroni anatsutsana naye Mose chifukwa cha mkazi mtundu wake Mkusi amene adamtenga; popeza adatenga mkazi Mkusi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Miriyamu ndi Aroni adayamba kumnena Mose chifukwa cha mkazi wachikusi amene Moseyo adamkwatira, poti adakwatiradi mkazi wa ku Kusi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Miriamu ndi Aaroni anayamba kuyankhula motsutsana ndi Mose chifukwa cha mkazi wa ku Kusi, popeza Moseyo anakwatira Mkusi. |
ndipo ndidzakulumbiritsa iwe pa Yehova, Mulungu wa Kumwamba, ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti usadzamtengere mwana wanga mkazi wa kwa ana aakazi a Akananiwo, amene ndikhala pakati pao.
Ndipo mbuyanga anandilumbiritsa ine kuti, Usamtengere mwana wanga mkazi wa ana aakazi a Kanani, m'dziko mwao m'mene ndikhala ine;
Ndipo anati Rebeka kwa Isaki, Ndalema moyo wanga chifukwa cha ana aakazi a Ahiti, akatenga Yakobo mkazi wa ana aakazi a Ahiti, onga ana aakazi a m'dziko lino, moyo wanga udzandikhalira ine bwanji?
Ndipo Farao anamutcha dzina la Yosefe Zafenati-Panea; ndipo anampatsa akwatire Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni. Ndipo Yosefe anatuluka wolamulira, nayendayenda m'dziko la Ejipito.
Ndipo wansembe wa Midiyani anali nao ana aakazi asanu ndi awiri, amene anadza kudzatunga madzi; ndipo anadzaza mimwero kuti amwetse gulu la atate wao.
Ndipo Mose anavomera kukhala naye munthuyo; ndipo anampatsa Mose mwana wake wamkazi Zipora.
ndipo ungatengereko ana ako aamuna ana ao akazi; nangachite chigololo ana ao aakazi potsata milungu yao, ndi kuchititsa ana anu amuna chigololo potsata milungu yao.
Mkazi wamasiye, kapena womleka, kapena woipsidwa, wachigololo, oterewa asawatenge; koma azitenga namwali wa anthu a mtundu wake akhale mkazi wake.
popeza anthu onse awa amene adaona ulemerero wanga, ndi zizindikiro zanga, ndidazichita mu Ejipito ndi m'chipululu, koma anandiyesa Ine kakhumi aka, osamvera mau anga;
ndipo anauka pamaso pa Mose, pamodzi ndi amuna mazana awiri mphambu makumi asanu a ana a Israele, ndiwo akalonga a khamulo, oitanidwa a msonkhano, amuna omveka.
Ndipo dzina lake la mkazi wake wa Amuramu ndiye Yokebede, mwana wamkazi wa Levi, wobadwira Levi mu Ejipito; ndipo iye anambalira Amuramu, Aroni ndi Mose, ndi Miriyamu mlongo wao.
Koma Iye anayankha, nati kwa iye wonenayo, Amai wanga ndani, ndipo abale anga ndi ayani?
Kumbukirani mau amene Ine ndinanena kwa inu, Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wake. Ngati anandilondalonda Ine, adzakulondalondani inunso; ngati anasunga mau anga, adzasunga anunso.