Chitatha ichi tsono iye anaumangira mzinda wa Davide linga lakunja, kumadzulo kwa Gihoni, m'chigwa, mpaka polowera pa Chipata cha Nsomba; nazinga Ofele, nalikweza kwambiri; anaikanso akazembe a nkhondo m'mizinda yonse yamalinga ya mu Yuda.
Nehemiya 3:3 - Buku Lopatulika Ndi Chipata cha Nsomba anachimanga ana a Hasena; anamanga mitanda yake, ndi kuika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipingiridzo yake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi chipata chansomba anachimanga ana a Hasena; anamanga mitanda yake, ndi kuika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipingiridzo yake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa A fuko la Hasena adamanga Chipata cha Nsomba. Iwowo adayala mitanda yake naikira zitseko zake, zotsekera zake, ndi mipiringidzo yake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chipata cha Nsomba chinamangidwanso ndi ana a fuko la Hasena. Iwo anayika mitanda yake ndi zitseko, zotsekera zake, ndi mipiringidzo yake. |
Chitatha ichi tsono iye anaumangira mzinda wa Davide linga lakunja, kumadzulo kwa Gihoni, m'chigwa, mpaka polowera pa Chipata cha Nsomba; nazinga Ofele, nalikweza kwambiri; anaikanso akazembe a nkhondo m'mizinda yonse yamalinga ya mu Yuda.
ndi pamwamba pa Chipata cha Efuremu, ndi ku Chipata Chakale, ndi ku Chipata cha Nsomba, ndi Nsanja ya Hananele, ndi Nsanja ya Zana, mpaka ku Chipata cha Nkhosa; ndipo anaima ku Chipata cha Akaidi.
ndi kalata kwa Asafu wosunga misitu ya mfumu, kuti andipatse mitengo ya mitanda ya kuzipata za linga lili ku Kachisi, ndi ya linga la mzinda, ndi ya nyumba imene ndidzalowamo ine. Ndipo mfumu inandipatsa monga mwa dzanja lokoma la Mulungu londikhalira.
Ndi pambali pao anakonza Meremoti mwana wa Uriya, mwana wa Hakozi. Ndi pambali pao anakonza Mesulamu mwana wa Berekiya, mwana wa Mesezabele. Ndi pambali pao anakonza Zadoki mwana wa Baana.
Ndi Chipata Chakale anachikonza Yoyada mwana wa Paseya; ndi Mesulamu mwana wa Besodeiya anamanga mitanda yake, ndi kuika zitseko zake, ndi zokowera zake, ndi mipingiridzo yake.
Kunali tsono, atamva Sanibalati, ndi Tobiya, ndi Gesemu Mwarabu, ndi adani athu otsala, kuti ndidatha kumanga lingali, posatsalaponso popasuka; (ngakhale pajapo sindinaike zitseko pazipata);
Ndipo atatha kumanga linga, ndinaika zitseko, nakhazika odikira, ndi oimbira, ndi Alevi;
Ndipo tsiku ilo, ati Yehova, kudzakhala phokoso lakulira lochokera ku Chipata cha Nsomba, ndi kuchema kochokera kudera lachiwiri, ndi kugamuka kwakukulu kochokera kuzitunda.