Nehemiya 2:8 - Buku Lopatulika8 ndi kalata kwa Asafu wosunga misitu ya mfumu, kuti andipatse mitengo ya mitanda ya kuzipata za linga lili ku Kachisi, ndi ya linga la mzinda, ndi ya nyumba imene ndidzalowamo ine. Ndipo mfumu inandipatsa monga mwa dzanja lokoma la Mulungu londikhalira. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 ndi kalata kwa Asafu wosunga misitu ya mfumu, kuti andipatse mitengo ya mitanda ya kuzipata za linga lili ku Kachisi, ndi ya linga la mudzi, ndi ya nyumba imene ndidzalowamo ine. Ndipo mfumu inandipatsa monga mwa dzanja lokoma la Mulungu londikhalira. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Mundipatsenso kalata ina yolembera Asafu, kapitao woyang'anira nkhalango ya mfumu, kuti akandipatse mitengo yokamangira mitanda ya zipata za linga loteteza Nyumba ya Mulungu, ya makoma a mzinda, ndiponso ya nyumba yokakhalamo ine.” Mfumu idandipatsa zimene ndidaapemphazo, popeza kuti Mulungu wanga wokoma mtima anali nane. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Mundipatsenso kalata yokapereka kwa Asafu woyangʼanira nkhalango ya mfumu, kuti akandipatse mitengo yokapangira mitanda ya zipata za nsanja yoteteza Nyumba ya Mulungu, mitanda ya khoma la mzinda ndi ya nyumba yokhalamo ine.” Mfumu indipatse zomwe ndinapempha popeza Yehova wokoma mtima anali nane. Onani mutuwo |