Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zefaniya 1:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo tsiku ilo, ati Yehova, kudzakhala phokoso lakulira lochokera ku Chipata cha Nsomba, ndi kuchema kochokera kudera lachiwiri, ndi kugamuka kwakukulu kochokera kuzitunda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo tsiku ilo, ati Yehova, kudzakhala phokoso lakulira lochokera kuchipata chansomba, ndi kuchema kochokera kudera lachiwiri, ndi kugamuka kwakukulu kochokera kuzitunda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Chauta akunena kuti, “Pa tsiku limenelo kulira kwakukulu kudzamveka ku Chipata cha Msika wa Nsomba; kulira kwakukuluko kudzamveka ku chigawo cham'kati cha mzinda wa Yerusalemu; kudzamvekanso kugunda kuchokera ku mapiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 “Pa tsiku limenelo,” akutero Yehova, “Kufuwula kwakukulu kudzamveka pa Chipata cha Nsomba, kulira kwa chisoni kuchokera mʼChigawo Chatsopano, ndi phokoso la kugumuka kochokera ku mapiri.

Onani mutuwo Koperani




Zefaniya 1:10
18 Mawu Ofanana  

Chinkana anatero Davide anathyola linga la Ziyoni, lomwelo ndilo mzinda wa Davide.


Ndipo Davide anakhala m'linga muja, nalitcha mzinda wa Davide. Davide namanga linga pozinga ponse kuyambira ku Milo ndi m'kati momwe.


Namuka Hilikiya wansembe, ndi Ahikamu, ndi Akibori, ndi Safani, ndi Asaya, kwa Hulida mneneri wamkazi, ndiye mkazi wa Salumu mwana wa Tikiva, mwana wa Harihasi, wosunga zovala za mfumu; analikukhala iye mu Yerusalemu m'dera lachiwiri, nalankhula naye.


Pamenepo Solomoni anayamba kumanga nyumba ya Yehova ku Yerusalemu, m'phiri la Moriya, kumene Mulungu anaonekera kwa Davide atate wake pamalo pamene Davide anakonzeratu pa dwale la Orinani Myebusi.


Momwemo Yehova analanditsa Hezekiya ndi okhala mu Yerusalemu m'dzanja la Senakeribu mfumu ya Asiriya, ndi m'dzanja la onse ena, nawatsogolera monsemo.


Chitatha ichi tsono iye anaumangira mzinda wa Davide linga lakunja, kumadzulo kwa Gihoni, m'chigwa, mpaka polowera pa Chipata cha Nsomba; nazinga Ofele, nalikweza kwambiri; anaikanso akazembe a nkhondo m'mizinda yonse yamalinga ya mu Yuda.


Namuka Hilikiya ndi iwo aja adawauza mfumu kwa Hulida mneneri wamkazi, mkazi wa Salumu mwana wa Tokati, mwana wa Hasira wosunga zovala, amene anakhala mu Yerusalemu m'dera lachiwiri, nanena naye mwakuti.


ndi pamwamba pa Chipata cha Efuremu, ndi ku Chipata Chakale, ndi ku Chipata cha Nsomba, ndi Nsanja ya Hananele, ndi Nsanja ya Zana, mpaka ku Chipata cha Nkhosa; ndipo anaima ku Chipata cha Akaidi.


Ndi Chipata cha Nsomba anachimanga ana a Hasena; anamanga mitanda yake, ndi kuika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipingiridzo yake.


Tonse tibangula ngati zilombo, ndi kulira maliro zolimba ngati nkhunda; tiyang'anira chiweruziro koma palibe; tiyang'anira chipulumutso koma chili patali ndi ife.


Chaka chakhumi ndi chimodzi cha Zedekiya, mwezi wachinai, tsiku lachisanu ndi chinai, mzinda unabooledwa.


Pakuti ndamva kubuula ngati kwa mkazi wobala, ndi msauko ngati wa mkazi wobala mwana wake woyamba, mau a mwana wamkazi wa Ziyoni wakupuma mosiyiza, wakutambasula manja ake, ndi kuti, Tsoka ine tsopano! Pakuti moyo wanga walefuka chifukwa cha ambanda.


Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pokhala ophedwa ao pakati pa mafano ao, pozinga maguwa ao a nsembe, pa zitunda zonse zazitali, pamwamba pa mapiri onse, ndi patsinde pa mitengo yogudira yonse, ndi patsinde pa thundu aliyense wagudugudu, pomwe adapereka zonunkhira zokoma kwa mafano ao onse.


Koma nyimbo za ku Kachisi zidzasanduka kubuma tsiku ilo, ati Ambuye Yehova; mitembo idzachuluka; adzaitaya paliponse padzakhala zii.


Tsikulo ndi tsiku la mkwiyo, tsiku la msauko ndi lopsinja tsiku la bwinja, ndi chipasuko, tsiku la mdima ndi la chisisira, tsiku la mitambo ndi lakuda bii;


Khala chete pamaso pa Ambuye Yehova; pakuti tsiku la Yehova liyandikira; pakuti Yehova wakonzeratu nsembe, anapatula oitanidwa ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa