Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zefaniya 1:11 - Buku Lopatulika

11 Chemani okhala m'chigwa, pakuti amalonda onse atayika, onsewo osenza siliva aonongeka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Chemani okhala m'chigwa, pakuti amalonda onse atayika, onsewo osenza siliva aonongeka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Inu okhala ku chigwa cha mzinda lirani komvetsa chisoni, chifukwa amalonda onse atha, onse ogulitsa siliva aonongeka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Lirani mwachisoni, inu amene mumakhala kumene kuli msika; a malonda anu onse adzapululidwa, ndiponso onse amene ali ndi siliva adzawonongedwa.

Onani mutuwo Koperani




Zefaniya 1:11
16 Mawu Ofanana  

Chinkana akundika ndalama ngati fumbi, ndi kukonzeratu zovala ngati dothi;


azikonzeretu, koma wolungama adzazivala, ndi wosalakwa adzagawa ndalamazo.


Kuwani, inu abusa, lirani, gubudukani, inu akulu a zoweta; pakuti masiku a kuphedwa kwanu akwanira ndithu, ndipo ndidzakuphwanyani inu, ndipo mudzagwa ngati chotengera chofunika.


Pamenepo, valani chiguduli, lirani ndi kubuula; pakuti mkwiyo wa kuopsa wa Yehova sunabwerere pa ife.


Fuula ndi kulira, wobadwa ndi munthu iwe, pakuti likhalira pa anthu anga, likhalira pa akalonga onse a Israele, laperekedwa kulupanga pamodzi ndi anthu anga; chifukwa chake panda pantchafu pako.


Pakuti taonani, anachokera chionongeko, koma Ejipito adzawasonkhanitsa, Mofi adzawaika m'manda; khwisa adzalanda zofunika zao zasiliva; minga idzakhala m'mahema mwao.


Mudzimangire chiguduli m'chuuno mwanu, nimulire, ansembe inu; bumani otumikira kuguwa la nsembe inu; lowani, gonani usiku wonse m'chiguduli, inu otumikira Mulungu wanga; pakuti nsembe yaufa ndi nsembe yothira zaletsedwera nyumba ya Mulungu wanu.


Galamukani, oledzera inu, nimulire; bumani, nonse akumwa vinyo, chifukwa cha vinyo watsopano; pakuti waletsedwa pakamwa panu.


Tsoka, okhala m'dziko la kunyanja, mtundu wa Akereti! Mau a Yehova atsutsana nawe, Kanani, dziko la Afilisti; ndidzakuononga, kuti pasakhale wokhala m'dziko.


Inde mbiya zonse za mu Yerusalemu ndi mu Yuda zidzakhala zopatulikira Yehova wa makamu; ndi onse akuphera nsembe adzafika nadzatengako, ndi kuphikamo; ndipo tsiku lomwelo simudzakhalanso Mkanani m'nyumba ya Yehova wa makamu.


nati kwa iwo akugulitsa nkhunda, Chotsani izi muno; musamayesa nyumba ya Atate wanga nyumba ya malonda.


Nanga tsono achuma inu, lirani ndi kuchema chifukwa cha masautso anu akudza pa inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa