Nehemiya 3:6 - Buku Lopatulika6 Ndi Chipata Chakale anachikonza Yoyada mwana wa Paseya; ndi Mesulamu mwana wa Besodeiya anamanga mitanda yake, ndi kuika zitseko zake, ndi zokowera zake, ndi mipingiridzo yake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Ndi chipata chakale anachikonza Yoyada mwana wa Paseya; ndi Mesulamu mwana wa Besodeiya anamanga mitanda yake, ndi kuika zitseko zake, ndi zokowera zake, ndi mipingiridzo yake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Yoyada, mwana wa Paseya, ndi Mesulamu mwana wa Besodeiya, adakonza Chipata Chakale. Adayala mitanda yake naikira zitseko zake, zotsekera zake ndi mipiringidzo yake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Chipata cha Yesana chinakonzedwa ndi Yoyada mwana wa Paseya ndi Mesulamu mwana wa Besodeya. Iwo anayika mitanda yake ndi kuyika zitseko, zotsekera zake ndi mipiringidzo yake. Onani mutuwo |