Pamene Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, Yehova anamuonekera Abramu nati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse; yenda iwe pamaso panga, nukhale wangwiro.
Mika 4:5 - Buku Lopatulika Pakuti mitundu yonse ya anthu idzayenda, wonse m'dzina la mulungu wake, ndipo ife tidzayenda m'dzina la Yehova Mulungu wathu kunthawi yonka muyaya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti mitundu yonse ya anthu idzayenda, wonse m'dzina la mulungu wake, ndipo ife tidzayenda m'dzina la Yehova Mulungu wathu kunthawi yonka muyaya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mitundu yonse ya anthu imayenda, uliwonse m'njira ya mulungu wake; koma ife tidzayenda m'njira ya Chauta, Mulungu wathu, mpaka muyaya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mitundu yonse ya anthu itha kutsatira milungu yawo; ife tidzayenda mʼnjira za Yehova Mulungu wathu mpaka muyaya. |
Pamene Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, Yehova anamuonekera Abramu nati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse; yenda iwe pamaso panga, nukhale wangwiro.
Koma a mtundu uliwonse anapanga milungu yaoyao, naiika m'nyumba za misanje adazimanga Asamariya, a mtundu uliwonse m'mizinda mwao mokhala iwo.
Mpaka lero lino achita monga mwa miyambo yoyambayi; saopa Yehova, sachita monga mwa malemba ao, kapena maweruzo ao, kapena chilamulo, kapena choikika adachilamulira Yehova ana a Yakobo, amene anamutcha Israele,
Tsopano ndidziwa kuti Yehova apulumutsa wodzozedwa wake; adzamvomereza mu Mwamba mwake moyera ndi mphamvu ya chipulumutso cha dzanja lake lamanja.
Pakuti Mulungu ameneyo ndiye Mulungu wathu kunthawi za nthawi, adzatitsogolera kufikira imfa.
Ndidzamuka mu mphamvu ya Ambuye Yehova; ndidzatchula chilungamo chanu, inde chanu chokha.
Yehova Mulungu wathu, pamodzi ndi Inu Ambuye ena adatilamulira ife; koma mwa Inu nokha tidzatchula dzina lanu.
Inde m'njira ya maweruziro anu, Yehova, ife talindira Inu; moyo wathu ukhumba dzina lanu, ndi chikumbukiro chanu.
ndipo ndidzapangana nao pangano lamuyaya, kuti sindidzawachokera kuleka kuwachitira zabwino; koma ndidzalonga kuopsa kwanga m'mitima yao, kuti asandichokere.
Potero muzimvera mau a Yehova Mulungu wanu, ndi kuchita malamulo ake ndi malemba ake, amene ndikuuzani lero lino.
Ndipo chilichonse mukachichita m'mau kapena muntchito, chitani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa Iye.
Ndipo ngati kutumikira Yehova kukuipirani mudzisankhire lero amene mudzamtumikira, kapena milungu imene anaitumikira makolo anu okhala tsidya lija la mtsinje, kapena milungu ya Aamori amene mukhala m'dziko lao; koma ine, ndi a m'nyumba yanga, tidzatumikira Yehova.