2 Mafumu 17:34 - Buku Lopatulika34 Mpaka lero lino achita monga mwa miyambo yoyambayi; saopa Yehova, sachita monga mwa malemba ao, kapena maweruzo ao, kapena chilamulo, kapena choikika adachilamulira Yehova ana a Yakobo, amene anamutcha Israele, Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201434 Mpaka lero lino achita monga mwa miyambo yoyambayi; saopa Yehova, sachita monga mwa malemba ao, kapena maweruzo ao, kapena chilamulo, kapena choikika adachilamulira Yehova ana a Yakobo, amene anamutcha Israele, Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa34 Akuchitabe zimene ankachita kale mpaka lero lino. Iwowo salemekeza Chauta kwenikweni ndipo satsata zogamula kapena zolengeza, ngakhale malangizo kapena malamulo amene Chauta adalamula zidzukulu za Yakobe, amene adamtchula kuti Israele. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero34 Mpaka lero lino iwo akupitirizabe kuchita zimene ankachita poyamba. Sapembedza Yehova kapenanso kutsata malangizo ake ndi malamulo ake, chiphunzitso chake monga mwa malamulo amene Yehova anawapereka kwa zidzukulu za Yakobo, amene anamutcha Israeli. Onani mutuwo |