Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 20:6 - Buku Lopatulika

6 Tsopano ndidziwa kuti Yehova apulumutsa wodzozedwa wake; adzamvomereza mu Mwamba mwake moyera ndi mphamvu ya chipulumutso cha dzanja lake lamanja.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Tsopano ndidziwa kuti Yehova apulumutsa wodzozedwa wake; adzamvomereza m'Mwamba mwake moyera ndi mphamvu ya chipulumutso cha dzanja lake lamanja.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Tsopano ndikudziŵa kuti Chauta adzathandiza wodzozedwa wake. Adzamuyankha ali ku malo ake oyera kumwamba, pakumpambanitsa kwathunthu ndi dzanja lake lamanja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Tsopano ndadziwa kuti Yehova amapulumutsa wodzozedwa wake; Iye amamuyankha kuchokera kumwamba ku malo ake opatulika ndi mphamvu yopulumutsa ya dzanja lake lamanja.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 20:6
19 Mawu Ofanana  

Ndipo mverani pembedzero la kapolo wanu ndi la anthu anu Aisraele, pamene adzapemphera molunjika kumalo kuno; ndipo mverani Inu mu Mwamba mokhala Inumo; ndipo pamene mukumva, khululukirani.


mverani Inu mu Mwamba mokhala Inu, ndipo chitani monga mwa zonse mlendoyo azipempha kwa Inu; kuti anthu onse a dziko lapansi adziwe dzina lanu, kuopa Inu, monga amatero anthu anu Aisraele, ndi kuti adziwe kuti nyumba ino ndaimangayi yatchedwa dzina lanu.


Onetsani chifundo chanu chodabwitsa, Inu wakupulumutsa okhulupirira Inu kwa iwo akuwaukira ndi dzanja lanu lamanja.


Ndipo mwandipatsa chikopa cha chipulumutso chanu; ndipo dzanja lamanja lanu landigwiriziza, ndipo chifatso chanu chandikuza ine.


Alanditsa mfumu yake ndi chipulumutso chachikulu; nachitira chifundo wodzozedwa wake, Davide, ndi mbumba yake, kunthawi zonse.


Adzikhazikitsa mafumu a dziko lapansi, nachita upo akulu pamodzi, Kutsutsana naye Yehova, ndi Wodzozedwa wake, ndi kuti,


Yehova ndiye mphamvu yao, inde mphamvu ya chipulumutso cha wodzozedwa wake.


Umo ndidziwa kuti mukondwera ndi ine, popeza mdani wanga sandiseka.


Amitundu anagwa m'mbuna imene anaikumba, lakodwa phazi lao muukonde anautchera.


Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.


Pamenepo udzaitana, ndipo Yehova adzayankha; udzafuula ndipo Iye adzati, Ndine pano. Ngati uchotsa pakati pa iwe goli, kukodolana moipa, ndi kulankhula moipa,


Tayang'anani kunsi kuchokera kumwamba, taonani pokhala panu poyera, ndi pa ulemerero wanu, changu chanu ndi ntchito zanu zamphamvu zili kuti? Mwanditsekerezera zofunafuna za mtima wanu ndi chisoni chanu.


Pakuti mitundu yonse ya anthu idzayenda, wonse m'dzina la mulungu wake, ndipo ife tidzayenda m'dzina la Yehova Mulungu wathu kunthawi yonka muyaya.


Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.


Potero, popeza anakwezedwa ndi dzanja lamanja la Mulungu, nalandira kwa Atate lonjezano la Mzimu Woyera, anatsanulira ichi, chimene inu mupenya nimumva.


Pamenepo lizindikiritse ndithu banja lililonse la Israele, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Khristu, Yesu amene inu munampachika.


zindikirani inu nonse, ndi anthu onse a Israele, kuti m'dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, amene inu munampachika pamtanda, amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa, mwa Iyeyu munthuyu aimirirapo pamaso panu, wamoyo.


Ameneyo Mulungu anamkweza ndi dzanja lake lamanja, akhale Mtsogoleri ndi Mpulumutsi, kuti apatse kwa Israele kulapa, ndi chikhululukiro cha machimo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa