Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 20:5 - Buku Lopatulika

5 Tidzafuula mokondwera mwa chipulumutso chanu, ndipo m'dzina la Mulungu wathu tidzakweza mbendera; Yehova akwaniritse mapempho ako onse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Tidzafuula mokondwera mwa chipulumutso chanu, ndipo m'dzina la Mulungu wathu tidzakweza mbendera; Yehova akwaniritse mapempho ako onse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Choncho tifuule ndi chimwemwe chifukwa chakuti mwapambana pa nkhondo, tikweze mbendera kutamanda dzina la Mulungu wathu. Chauta akupatse zonse zimene wapempha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Ife tidzafuwula ndi chimwemwe pamene iwe wapambana ndipo tidzanyamula mbendera zathu mʼdzina la Mulungu wathu, Yehova ayankhe zopempha zako zonse.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 20:5
19 Mawu Ofanana  

M'mahema a olungama muli liu lakufuula mokondwera Dzanja lamanja la Yehova ndi la chipulumutso:


Koma ine ndakhulupirira pa chifundo chanu; mtima wanga udzakondwera nacho chipulumutso chanu.


Muyeso wao wapitirira padziko lonse lapansi, ndipo mau ao ku malekezero a m'dziko muli anthu. Iye anaika hema la dzuwa m'menemo,


Yehova, adzasekera mfumu mu mphamvu yanu; adzakondwera kwakukulu m'chipulumutso chanu!


Pakuti mufika kwa iye ndi madalitso okoma; muika korona wa golide woyengetsa pamutu pake.


Ndipo moyo wanga udzakondwera mwa Yehova; udzasekera mwa chipulumutso chake.


Koma mwapatsa mbendera akuopa Inu, aikweze chifukwa cha choonadi.


Kuti ndibukitse lemekezo lanu lonse; pa bwalo la mwana wamkazi wa Ziyoni, ndidzakondwera nacho chipulumutso chanu.


Ndipo Mose anamanga guwa la nsembe, nalitcha dzina lake Yehova Nisi:


Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti muzu wa Yese umene uima ngati mbendera ya mitundu ya anthu, amitundu adzafunafuna uwu; ndipo popuma pake padzakhala ulemerero.


Ndipo adzanena tsiku limenelo, Taonani, uyu ndiye Mulungu wathu; tamlindirira Iye, adzatipulumutsa; uyu ndiye Yehova, tamlindirira Iye, tidzakondwa ndi kusekerera m'chipulumutso chake.


Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Iye wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo.


Pakuti mitundu yonse ya anthu idzayenda, wonse m'dzina la mulungu wake, ndipo ife tidzayenda m'dzina la Yehova Mulungu wathu kunthawi yonka muyaya.


koma ndidzakondwera mwa Yehova, ndidzasekerera mwa Mulungu wa chipulumutso changa.


ndipo mzimu wanga wakondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga,


Pamenepo Eli anayankha nati, Pita ndi mtendere; ndipo Mulungu wa Israele akupatse chopempha chako unachipempha kwa Iye.


Ndipo Davide anati kwa Mfilistiyo, Iwe ukudza kwa ine ndi lupanga, ndi mkondo, ndi nthungo; koma ine ndafika kwa iwe m'dzina la Yehova wa makamu, Mulungu wa ankhondo a Israele amene iwe unawanyoza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa