mpaka Yehova adachotsa Israele pamaso pake, monga adanena mwa dzanja la atumiki ake onse aneneriwo. Momwemo Israele anachotsedwa m'dziko lao kunka nao ku Asiriya mpaka lero lino.
Mika 2:5 - Buku Lopatulika Chifukwa chake udzasowa woponya chingwe chamaere m'msonkhano wa Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake udzasowa woponya chingwe chamaere m'msonkhano wa Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono pa nthaŵi imene Chauta adzabwezeranso dziko kwa anthu ake, inuyo simudzalandirako gawo lililonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nʼchifukwa chake simudzakhala ndi munthu mu msonkhano wa Yehova kuti agawe dziko pochita maere. |
mpaka Yehova adachotsa Israele pamaso pake, monga adanena mwa dzanja la atumiki ake onse aneneriwo. Momwemo Israele anachotsedwa m'dziko lao kunka nao ku Asiriya mpaka lero lino.
Ndipo okwera kuchokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adoni, ndi Imeri, ndi awa; koma sanakhoze kutchula nyumba za makolo ao, kapena mbumba zao, ngati ali a Israele;
Sadzakhala m'dziko la Yehova; koma Efuremu adzabwerera kunka ku Ejipito; ndipo adzadya chakudya chodetsa mu Asiriya.
Ndipo Mose anauza ana a Israele, nati, Ili ndi dzikoli mudzalandira ndi kuchita maere, limene Yehova analamulira awapatse mafuko asanu ndi anai ndi hafu;
Mwana wa m'chigololo asalowe m'msonkhano wa Yehova, ngakhale mbadwo wake wakhumi usalowe m'msonkhano wa Yehova.
Pamene Wam'mwambamwamba anagawira amitundu cholowa chao, pamene anagawa ana a anthu, anaika malire a mitundu ya anthu, monga mwa kuwerenga kwao kwa ana a Israele.
Ndipo Yoswa anawalotera maere ku Silo pamaso pa Yehova; ndi apo Yoswa anawagawira ana a Israele dziko, monga mwa magawo ao.
Mudzifunire amuna, fuko lililonse amuna atatu; kuti ndiwatume, anyamuke, nayendeyende iwo pakati padziko, nalilembe monga mwa cholowa chao; nabwerenso kwa ine.