Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 18:4 - Buku Lopatulika

4 Mudzifunire amuna, fuko lililonse amuna atatu; kuti ndiwatume, anyamuke, nayendeyende iwo pakati padziko, nalilembe monga mwa cholowa chao; nabwerenso kwa ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Mudzifunire amuna, fuko lililonse amuna atatu; kuti ndiwatume, anyamuke, nayendeyende iwo pakati pa dziko, nalilembe monga mwa cholowa chao; nabwerenso kwa ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Tandipatsani amuna atatu a fuko lililonse. Ameneŵa ndiŵatuma kuti akayendere dziko lonselo, ndipo alembe bwino magawo ake onse, kuti tithandizidwe poligaŵa. Atatero, abwererenso kuno kwa ine.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Sankhani amuna atatu kuchokera ku fuko lililonse ndipo ine ndidzawatuma kuti akayendere dzikolo ndi kukalilembera bwino kuti ndiligawe kukhala lawo. Akatero, abwererenso kwa ine.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 18:4
9 Mawu Ofanana  

Chifukwa chake udzasowa woponya chingwe chamaere m'msonkhano wa Yehova.


Ndipo pamodzi ndi inu pakhale munthu mmodzi wa mafuko onse; yense mkulu wa nyumba ya kholo lake.


Udzitumire amuna, kuti azonde dziko la Kanani, limene ndilikupatsa ana a Israele; utumize munthu mmodzi wa fuko lililonse la makolo ao, yense kalonga pakati pa anzake.


Ndipo Yoswa anati kwa ana a Israele, Muchedwa mpaka liti kulowa ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu anakupatsani?


Ndipo adzaligawa magawo asanu ndi awiri; Yuda adzakhala m'malire ake kumwera, ndi a m'nyumba ya Yosefe adzakhala m'malire mwao kumpoto.


Ndipo muzilemba dziko likhale magawo asanu ndi awiri, ndi kubwera nao kuno kwa ine malembo ake; ndipo ndidzakuloterani maere pano pamaso pa Yehova Mulungu wathu.


Namuka amunawo, napitapita pakati padziko, nalilemba m'buku, nayesa midzi yake, magawo asanu, nabwera kwa Yoswa ku chigono ku Silo.


Ndipo tsono, mudzitengere amuna khumi ndi awiri mwa mafuko a Israele, fuko limodzi mwamuna mmodzi.


Mudzitengere mwa anthu, amuna khumi ndi awiri, fuko limodzi mwamuna mmodzi;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa