Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Mika 2:12 - Buku Lopatulika

Ndidzakumemezani ndithu, Yakobo, inu nonse; ndidzasonkhanitsa ndithu otsala a Israele; ndidzawaika pamodzi ngati nkhosa za ku Bozira; ngati zoweta pakati pa busa pao adzachita phokoso chifukwa cha kuchuluka anthu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndidzakumemezani ndithu, Yakobo, inu nonse; ndidzasonkhanitsa ndithu otsala a Israele; ndidzawaika pamodzi ngati nkhosa za ku Bozira; ngati zoweta pakati pa busa pao adzachita phokoso chifukwa cha kuchuluka anthu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

“Koma inu banja lonse la Yakobe, ndidzakusonkhanitsani. Onse otsala a ku Israele ndidzaŵasonkhanitsa pamodzi ngati nkhosa m'khola, ngati gulu la zoŵeta pa busa lake. Malowo adzakhala thithithi ndi chinamtindi cha anthu.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“Inu banja la Yakobo, ndidzakusonkhanitsani nonse; ndidzawasonkhanitsa pamodzi otsala a ku Israeli. Ndidzawabweretsa pamodzi ngati nkhosa mʼkhola, ngati ziweto pa msipu wake; malowo adzadzaza ndi chinamtindi cha anthu.

Onani mutuwo



Mika 2:12
28 Mawu Ofanana  

Ndipo Bela anamwalira, ndipo Yobabu mwana wamwamuna wa Zera wa ku Bozira analamulira m'malo mwake.


Ndipo anafa Bela; ndi Yobabu mwana wa Zera wa ku Bozira anakhala mfumu m'malo mwake.


Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti Ambuye adzabweza kachiwiri ndi dzanja lake anthu ake otsala ochokera ku Asiriya, ndi ku Ejipito, ndi ku Patirosi, ndi ku Kusi, ndi ku Elamu, ndi ku Sinara, ndi ku Hamati, ndi ku zisumbu za m'nyanja.


Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti Yehova adzaomba tirigu wake, kuchokera madzi a nyanja, kufikira kumtsinje wa Ejipito, ndipo mudzakunkhidwa mmodzi, inu ana a Israele.


Lupanga la Yehova lakhuta ndi mwazi, lanona ndi mafuta ndi mwazi wa anaankhosa, ndi mbuzi, ndi mafuta a impso ya nkhosa zamphongo; pakuti Yehova ali ndi nsembe mu Bozira, ndi ophedwa ambiri m'dziko la Edomu.


Pamenepo anaankhosa adzadyapo ngati m'busa mwao, ndi malo a bwinja a zonenepa zachilendo zidzadyapo.


Ndipo ndidzasonkhanitsa zotsala za zoweta zanga za m'maiko onse m'mene ndinazipirikitsiramo, ndipo ndidzazitengeranso kumakola ao; ndipo zidzabalana ndi kuchuluka.


Masiku omwewo nyumba ya Yuda idzayenderena ndi nyumba ya Israele, ndipo adzatuluka pamodzi kudziko la kumpoto kunka ku dziko limene ndinapatsa makolo anu kuti alowemo.


Pakuti atero Ambuye Yehova, Taonani, Ine, Inedi ndidzapwaira nkhosa zanga ndi kuzifunafuna.


Ndipo ndidzazitulutsa mwa mitundu ya anthu, ndi kuzisonkhanitsa m'maiko, ndi kulowa nazo m'dziko lao; ndipo ndidzazidyetsa pa mapiri a Israele, patimitsinje, ndi ponse pokhala anthu m'dziko.


chifukwa chake ndidzapulumutsa gulu langa lisakhalenso chakudya; ndipo ndidzaweruza pakati pa zoweta ndi zoweta.


Ndipo inu nkhosa zanga, nkhosa zapabusa panga, ndinu anthu, ndi Ine ndine Mulungu wanu, ati Ambuye Yehova.


Atero Ambuye Yehova, Ichi chomwe adzandipempha a nyumba ya Israele ndiwachitire ichi, ndidzawachulukitsira anthu ngati nkhosa.


Nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndidzatenga ana a Israele pakati pa amitundu kumene adankako, ndi kuwasokolotsa kumbali zonse, ndi kulowa nao m'dziko mwao;


Ndipo ana a Yuda ndi ana a Israele adzasonkhanidwa pamodzi, nadzadziikira mkulu mmodzi, nadzakwera kuchoka m'dziko; pakuti tsiku la Yezireele ndi lalikulu.


koma ndidzatumiza moto pa Temani, udzanyeketsa nyumba zachifumu za Bozira.


Wothyola wakwera pamaso pao; iwo anathyola, napita kuchipata, natuluka pomwepo; ndi mfumu yao yapita pamaso pao, ndipo Yehova awatsogolera.


Ndipo iwe, nsanja ya nkhosa, chitunda cha mwana wamkazi wa Ziyoni, udzafikira iwe, inde udzafika ulamuliro wakale, ufumu wa mwana wamkazi wa Yerusalemu.


Ndipo otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mame ochokera kwa Yehova ngati mvula paudzu, yosachedwera munthu, yosalindira ana a anthu.


Ndipo otsala a Yakobo adzakhala mwa amitundu, pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mkango mwa nyama zakuthengo, ngati msona wa mkango mwa magulu a nkhosa; umenewo ukapitako, upondereza, numwetula, ndipo palibe wakupulumutsa.


Mudyetse anthu anu ndi ndodo yanu, nkhosa za cholowa chanu zokhala pazokha m'nkhalango pakati pa Karimele, zidye mu Basani ndi mu Giliyadi masiku a kale lomwe.


Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakukhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a cholowa chake? Sasunga mkwiyo wake kunthawi yonse popeza akondwera nacho chifundo.


Nthawi yomweyo ndidzakulowetsani, ndi nthawi yomweyo ndidzakusonkhanitsani; pakuti ndidzakuikani mukhale dzina, ndi chilemekezo mwa mitundu yonse ya anthu a padziko lapansi, pamene ndibweza undende wanu pamaso panu, ati Yehova.