Mika 5:7 - Buku Lopatulika7 Ndipo otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mame ochokera kwa Yehova ngati mvula paudzu, yosachedwera munthu, yosalindira ana a anthu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Ndipo otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mame ochokera kwa Yehova ngati mvula paudzu, yosachedwera munthu, yosalindira ana a anthu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Onse otsalira a Yakobe adzakhala dalitso pakati pa mitundu yambiri ya anthu ngati mame ochoka kwa Chauta. Adzakhala ngati mvula yowaza pa udzu, imene sichita kulamulidwa ndi anthu, siidikira lamulo la munthu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Otsalira a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu ngati mame ochokera kwa Yehova, ngati mvumbi pa udzu, omwe sulamulidwa ndi munthu kapena kudikira lamulo la anthu. Onani mutuwo |
Ndipo ndidzaika chizindikiro pakati pao, ndipo ndidzatumiza onse amene apulumuka mwa iwo kwa amitundu, kwa Tarisisi, kwa Puti ndi kwa Aludi, okoka uta kwa Tubala ndi Yavani, kuzisumbu zakutali, amene sanamve mbiri yanga, ngakhale kuona ulemerero wanga; ndipo adzabukitsa ulemerero wanga pakati pa amitundu.