Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mika 5:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo iwo adzatha dziko la Asiriya ndi lupanga, ndi dziko la Nimirodi, ndilo polowera pake; ndipo adzatilanditsa kwa a ku Asiriya pamene alowa m'dziko lathu, pamene aponda m'kati mwa malire athu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo iwo adzatha dziko la Asiriya ndi lupanga, ndi dziko la Nimirodi, ndilo polowera pake; ndipo adzatilanditsa kwa a ku Asiriya pamene alowa m'dziko lathu, pamene aponda m'kati mwa malire athu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Iwowo adzagonjetsa dziko la Asiriya ndi lupanga, dziko la Nimirodi adzalilamulira mwankhondo. Adzatipulumutsa kwa Aasiriya, iwowo akadzakaloŵa m'dziko mwathu, kudzatithira nkhondo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Iwo adzagonjetsa dziko la Asiriya ndi lupanga, dziko la Nimurodi adzalilamulira mwankhondo. Adzatipulumutsa kwa Asiriya akadzafika mʼmalire a mʼdziko lathu kudzatithira nkhondo.

Onani mutuwo Koperani




Mika 5:6
26 Mawu Ofanana  

Masiku a Peka mfumu ya Israele anadza Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, nalanda Iyoni, ndi Abele-Beti-Maaka, ndi Yanowa, ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Giliyadi, ndi Galileya, dziko lonse la Nafutali; nawatenga andende kunka nao ku Asiriya.


Ndi Kusi anabala Nimirodi; iye anayamba kukhala wamphamvu padziko.


Motero Yehova anawafikitsira akazembe a khamu la nkhondo la mfumu ya Asiriya, namgwira Manase ndi zokowera, nammanga matangadza, namuka naye ku Babiloni.


Nditanena mau anga sanalankhulenso, ndi kunena kwanga kunawakhera.


Anthu anu adzadzipereka eni ake tsiku la chamuna chanu: M'moyera mokometsetsa, mobadwira matanda kucha, muli nao mame a ubwana wanu.


Adzanga mvula yakugwa pa udzu wosenga, monga mvula yothirira dziko.


Ndipo mitundu ya anthu idzawatenga, ndi kuwafikitsa kumalo a kwao; ndipo a nyumba ya Israele adzakhala nao amitunduwo m'dziko la Yehova, ndi kuwayesa atumiki ndi adzakazi, ndipo amitunduwo adzatengedwa ndende, ndi amenewo anali ndende zao; ndipo Aisraele adzalamulira owavuta.


kuti Ine ndidzathyola Aasiriya m'dziko langa, ndi pamwamba pa mapiri anga ndidzawapondereza; pomwepo goli lake lidzachoka pa iwo, ndi katundu wake adzachoka paphewa pao.


Tsoka kwa iwe amene usakaza, chinkana sunasakazidwe; nupangira chiwembu, chinkana sanakupangire iwe chiwembu! Utatha kusakaza, iwe udzasakazidwa; ndipo utatha kupangira chiwembu, iwo adzakupangira iwe chiwembu.


Ndipo mthenga wa Yehova anatuluka, naphaipha m'zithando za Asiriya, zikwi zana ndi makumi asanu ndi atatu ndi zisanu, ndipo pamene anthu anauka mamawa, taonani, onse ndiwo mitembo.


Ndipo Senakeribu, mfumu ya Asiriya, anachoka, namuka, nabwerera, nakhala pa Ninive.


Ndipo likatsala limodzi la magawo khumi m'menemo, lidzadyedwanso; monga kachere, ndi monganso thundu, imene tsinde lake likhalabe ataigwetsa; chotero mbeu yopatulika ndiyo tsinde lake.


Mwa zachabe za mitundu ya anthu zilipo kodi, zimene zingathe kuvumbitsa mvula? Kapena miyamba kubweretsa mivumbi? Kodi si ndinu, Yehova, Mulungu wathu? Ndipo tidzakudikirani Inu; pakuti munalenga zonse zimenezi.


Ili kuti ngaka ya mikango, ndi podyera misona ya mikango, kumene mkango, waumuna ndi waukazi, ukayenda ndi mwana wa mkango, kopanda wakuiposa?


Ndipo adzatambasulira dzanja lake kumpoto nadzaononga Asiriya, nadzasanduliza Ninive akhale bwinja, wouma ngati chipululu.


Koma ndidzasiya pakati pako anthu ozunzika ndi osauka, ndipo iwo adzakhulupirira dzina la Yehova.


chipulumutso cha adani athu, ndi padzanja la anthu onse amene atida ife.


Kutipatsa ife kuti titalanditsidwa kudzanja la adani athu, tidzamtumikira Iye, opanda mantha,


Ndipo anayamba kwa Mose, ndi kwa aneneri onse nawatanthauzira iwo m'malembo onse zinthu za Iye yekha.


Chiphunzitso changa chikhale ngati mvula; maneno anga agwe ngati mame; ngati mvula yowaza pamsipu, ndi monga madontho a mvula pazitsamba.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa