Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mika 5:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo otsala a Yakobo adzakhala mwa amitundu, pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mkango mwa nyama zakuthengo, ngati msona wa mkango mwa magulu a nkhosa; umenewo ukapitako, upondereza, numwetula, ndipo palibe wakupulumutsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo otsala a Yakobo adzakhala mwa amitundu, pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mkango mwa nyama zakuthengo, ngati msona wa mkango mwa magulu a nkhosa; umenewo ukapitako, upondereza, numwetula, ndipo palibe wakupulumutsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Onse otsalira a Yakobe adzakhala temberero pakati pa mitundu ya anthu, ngati mkango pakati pa nyama zam'nkhalango. Adzakhala ngati mwana wa mkango, pakati pa gulu la nkhosa, amene amati akadzaziloŵerera, amazimbwandira ndi kuzikadzula. Ndipo sipakhala wozipulumutsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu ya anthu, mʼgulu la anthu a mitundu yambiri, ngati mkango pakati pa nyama za mʼnkhalango. Ngati mwana wa mkango pakati pa gulu la nkhosa, amene pozidutsa amazidya ndi kuzikhadzula, ndipo palibe angathe kuzilanditsa.

Onani mutuwo Koperani




Mika 5:8
29 Mawu Ofanana  

Yuda ndi mwana wa mkango, kuchokera kuzomotola, mwananga, wakwera; anawerama pansi, anabwatama ngati mkango, ndipo ngati mkango waukazi; ndani adzamukitsa iye?


Muika mdima ndipo pali usiku; pamenepo zituluka zilombo zonse za m'thengo.


Mwa Inu tidzakankhira pansi otsutsana nafe, m'dzina lanu tidzapondereza akutiukira ife.


Dziwitsani ichi inu oiwala Mulungu, kuti ndingakumwetuleni, ndipo mungasowepo mpulumutsi.


Mkango umene uposa zilombo kulimba, supatukira chinthu chilichonse;


kubangula kwao kudzafanana ndi mkango, iwo adzabangula ngati ana a mikango, inde iwo adzabangula, nadzagwira nyama, naichotsa bwino opanda wakupulumutsa.


osatenga nkhuni kuthengo, kapena kuzitema kunkhalango; popeza adzasonkha moto ndi zidazo; nadzafunkha iwo amene anawafunkha, ndi kulanda zao za iwo adalanda zaozo, ati Ambuye Yehova.


Pakuti ndidzakhala kwa Efuremu ngati mkango, ndi kwa nyumba ya Yuda ngati msona wa mkango; ndidzamwetula Ine ndi kuchoka; ndidzanyamula, ndipo palibe wakulanditsa.


Ndidzakumemezani ndithu, Yakobo, inu nonse; ndidzasonkhanitsa ndithu otsala a Israele; ndidzawaika pamodzi ngati nkhosa za ku Bozira; ngati zoweta pakati pa busa pao adzachita phokoso chifukwa cha kuchuluka anthu.


Nyamuka nupunthe, mwana wamkazi wa Ziyoni; pakuti ndidzasanduliza nyanga yako ikhale yachitsulo, ndi ziboda zako zikhale zamkuwa; ndipo udzaphwanya mitundu yambiri ya anthu; ndipo uzipereka chiperekere phindu lao kwa Yehova, ndi chuma chao kwa Ambuye wa dziko lonse lapansi.


ndipo wotsimphinayo ndidzamuyesa wotsala, ndi iye wotayidwa kutali mtundu wamphamvu; ndipo Yehova adzakhala mfumu yao m'phiri la Ziyoni kuyambira pamenepo kufikira kosatha.


Chifukwa chake Iye adzawapereka kufikira nthawi yoti wobalayo wabala; pamenepo otsala a abale ake adzabwera pamodzi ndi ana a Israele.


Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakukhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a cholowa chake? Sasunga mkwiyo wake kunthawi yonse popeza akondwera nacho chifundo.


Ndipo adzakhala ngati ngwazi zakupondereza adani m'thope la kubwalo kunkhondo; ndipo adzachita nkhondo, chifukwa Yehova ali nao; ndi apakavalo adzachitidwa manyazi.


Pakuti sindidzachitiranso chifundo okhala m'dzikomo, ati Yehova; koma taonani, ndidzapereka anthu, yense m'dzanja la mnansi wake, ndi m'dzanja la mfumu yake; ndipo iwo adzakantha dzikoli, ndi m'dzanja mwao sindidzawalanditsa.


Ndipo kudzachitika tsiku ilo, ndidzaika Yerusalemu akhale mwala wolemetsa mitundu yonse ya anthu; onse akuusenza adzadzilasa nao; ndi amitundu onse a padziko lapansi adzasonkhana kutsutsana nao.


Ndipo banja la ku Ejipito likapanda kukwera, losafika, sudzawagwera kodi mliri umene Yehova adzakantha nao amitundu osakwera kusunga chikondwerero cha Misasa?


Yehova wa makamu adzawatchinjiriza; ndipo adzadza, nadzapondereza miyala yoponyera; ndipo adzamva, nadzachita phokoso ngati avinyo; ndipo adzadzazidwa ngati mbale, ngati ngodya za guwa la nsembe.


Ndipo mudzapondereza oipa; pakuti adzakhala ngati mapulusa kumapazi anu, tsiku ndidzaikalo, ati Yehova wa makamu.


Anaunthama, nagona pansi ngati mkango, ngati mkango waukazi; adzamuutsa ndani? Wodalitsika aliyense wakudalitsa iwe, wotemberereka aliyense wakutemberera iwe.


Ndipo yemwe sadzakulandirani inu kapena kusamva mau anu, pamene mulikutuluka m'nyumbayo, kapena m'mudzimo, sansani fumbi m'mapazi anu.


Koma pamene iwo, anamkana, nachita mwano, anakutumula malaya ake, nati kwa iwo, Mwazi wanu ukhale pa mitu yanu; ine ndilibe kanthu; kuyambira tsopano ndinka kwa amitundu.


Penyani musakane wolankhulayo. Pakuti ngati iwowa sanapulumuke, pomkana Iye amene anawachenjeza padziko, koposatu sitidzapulumuka ife, odzipatulira kwa Iye wa Kumwamba;


tidzapulumuka bwanji ife, tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotero? Chimene Ambuye adayamba kuchilankhula, ndipo iwo adachimva anatilimbikitsira ife;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa