Mika 7:14 - Buku Lopatulika14 Mudyetse anthu anu ndi ndodo yanu, nkhosa za cholowa chanu zokhala pazokha m'nkhalango pakati pa Karimele, zidye mu Basani ndi mu Giliyadi masiku a kale lomwe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 Mudyetse anthu anu ndi ndodo yanu, nkhosa za cholowa chanu zokhala pa zokha m'nkhalango pakati pa Karimele, zidye m'Basani ndi m'Giliyadi masiku a kale lomwe. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 Inu Chauta muŵatsogolere anthu anu ndi ndodo yanu yoŵatetezera, muŵete nkhosa zanu zimene mudazisankha. Tsopano zikukhala zokha m'nkhalango pakati pa dziko la chonde. Koma muzilole kuti zikadye ku busa labwino, ku Basani ndi Giliyadi, monga masiku akale. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 Wetani anthu anu ndi ndodo yanu yowateteza, nkhosa zimene ndi cholowa chanu, zimene zili zokha mʼnkhalango, mʼdziko la chonde. Muzilole kuti zidye mu Basani ndi mu Giliyadi monga masiku akale. Onani mutuwo |