Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mika 7:13 - Buku Lopatulika

13 Koma dziko lidzakhala labwinja chifukwa cha iwo okhalamo, mwa zipatso za machitidwe ao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Koma dziko lidzakhala labwinja chifukwa cha iwo okhalamo, mwa zipatso za machitidwe ao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Koma dziko lapansi lidzasanduka chipululu chifukwa cha zoipa za anthu ake. Amenewo ndiwo malipiro a ntchito zao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Dziko lapansi lidzasanduka chipululu chifukwa cha anthu okhala mʼdzikomo, potsatira zochita za anthuwo.

Onani mutuwo Koperani




Mika 7:13
22 Mawu Ofanana  

Monga umo, ndaonera, olimira mphulupulu, nabzala vuto, akololapo zomwezo.


momwemo adzadya zipatso za mayendedwe ao, nadzakhuta zolingalira zao.


Mumpatse zipatso za manja ake; ndi ntchito zake zimtame kubwalo.


Zoipa zakezake zidzagwira woipa; adzamangidwa ndi zingwe za uchimo wake.


Tsiku limenelo mizinda yake yolimba idzakhala ngati mabwinja a m'nkhalango, ndi a pansonga paphiri, osiyidwa pamaso pa ana a Israele; ndipo padzakhala bwinja.


Ine Yehova ndisanthula mtima, ndiyesa impso, kuti ndimpatse munthu yense monga mwa njira zake, monga zipatso za ntchito zake.


Ndipo ndidzakulangani inu monga mwa chipatso cha ntchito zanu, ati Yehova; ndipo ndidzayatsa moto m'nkhalango mwake, ndipo udzatha zonse zomzungulira iye.


Ndipo dziko lonseli lidzakhala labwinja, ndi chizizwitso, ndipo mitundu iyi idzatumikira mfumu ya ku Babiloni zaka makumi asanu ndi awiri.


wamkulu mu upo, wamphamvu m'ntchito; maso anu ali otsegukira njira zonse za ana a anthu; kuti mupatse yense monga mwa chipatso cha machitidwe ake;


nunene kwa anthu a m'dziko, Atero Yehova Mulungu za iwo okhala mu Yerusalemu, ndi za dziko la Israele, Adzadya mkate wao ndi nkhawa, ndi kumwa madzi ao ndi kusumwa; pakuti dziko lao lidzakhala lachipululu, kuleka kudzala kwake chifukwa cha chiwawa cha onse okhalamo.


Ndipo ndidzasanduliza dziko likhale lachipululu ndi lodabwitsa, ndi mphamvu yake yodzikuza idzatha, ndi mapiri a Israele adzakhala achipululu, osapitako munthu.


Momwemo Ziyoni adzalimidwa ngati munda chifukwa cha inu, ndi mu Yerusalemu mudzasanduka miunda, ndi phiri la nyumba ngati misanje ya m'nkhalango.


Pamenepo adzafuulira kwa Yehova, koma sadzawayankha; inde, adzawabisira nkhope yake nthawi yomweyo, monga momwe anaipsa machitidwe ao.


Chifukwa chake Iye adzawapereka kufikira nthawi yoti wobalayo wabala; pamenepo otsala a abale ake adzabwera pamodzi ndi ana a Israele.


Chifukwa chake Inenso ndakukantha ndi kukupweteketsa; ndakupulula chifukwa cha zochimwa zako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa