Zefaniya 3:20 - Buku Lopatulika20 Nthawi yomweyo ndidzakulowetsani, ndi nthawi yomweyo ndidzakusonkhanitsani; pakuti ndidzakuikani mukhale dzina, ndi chilemekezo mwa mitundu yonse ya anthu a padziko lapansi, pamene ndibweza undende wanu pamaso panu, ati Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201420 Nthawi yomweyo ndidzakulowetsani, ndi nthawi yomweyo ndidzakusonkhanitsani; pakuti ndidzakuikani mukhale dzina, ndi chilemekezo mwa mitundu yonse ya anthu a pa dziko lapansi, pamene ndibweza undende wanu pamaso panu, ati Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa20 Nthaŵi imeneyo ndidzakusonkhanitsani, Ndidzakubwezerani kwanu. Ndidzakusandutsani otchuka ndi olemekezeka, pakati pa anthu a mitundu yonse ya pa dziko lapansi. Ndidzakubwezerani ufulu wanu inu mukupenya. Ndatero Ine Chauta.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero20 Pa nthawi imeneyo ndidzakusonkhanitsani; pa nthawi imeneyo ndidzakubweretsani ku mudzi kwanu. Ndidzakuyamikirani ndi kukuchitirani ulemu pakati pa mitundu ya anthu a dziko lapansi pamene ndidzabwezeretsa mtendere wanu inu mukuona,” akutero Yehova. Onani mutuwo |