Ndi a ana a Isakara, anthu akuzindikira nyengo, akudziwa zoyenera Israele kuzichita, akulu ao ndiwo mazana awiri; ndi abale ao onse anapenyerera pakamwa pao.
Mateyu 16:3 - Buku Lopatulika Ndipo m'mawa, Lero nkwa mphepo: popeza thambo lili la cheza chodera. Mudziwa kuzindikira za pa nkhope ya thambo; koma zizindikiro za nyengo ino, simungathe kuzindikira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo m'mawa, Lero nkwa mphepo: popeza thambo lili la cheza chodera. Mudziwa kuzindikira za pa nkhope ya thambo; koma zizindikiro za nyengo yino, simungathe kuzindikira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo m'maŵa mumati, ‘Lero ndiye kugwa mvula yamkuntho, popeza kuti kumwambaku kwachita mitambo yabii.’ Mumatha kutanthauzira m'mene kukuwonekera kumwambaku, koma osatha kutanthauzira zizindikiro za nthaŵi zino. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo mmawa mumati, ‘Lero kudzakhala mvula yamphepo popeza thambo ndi lofiira ndi mitambo ya mvula.’ Inu mumadziwa kutanthauzira maonekedwe a thambo koma simungathe kutanthauzira zizindikiro za nthawi. |
Ndi a ana a Isakara, anthu akuzindikira nyengo, akudziwa zoyenera Israele kuzichita, akulu ao ndiwo mazana awiri; ndi abale ao onse anapenyerera pakamwa pao.
akhungu alandira kuona kwao, ndi opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ndi ogontha akumva, ndi akufa aukitsidwa, ndi kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino.
Koma tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pao; pakuti inu nokha simulowamo, ndipo muwaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo.
Ndipo Yesu anayendayenda mu Galileya monse, analikuphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu, nachiritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu.
Wonyenga iwe! Tayamba kuchotsa m'diso lako mtandawo, ndipo pomwepo udzapenyetsa kuchotsa kachitsotso m'diso la mbale wako.
Tsoka inu! Chifukwa muli ngati manda osaoneka, ndipo anthu akuyendayenda pamwamba pao sadziwa.
Onyenga inu, mudziwa kuzindikira nkhope yake ya dziko lapansi ndi ya thambo; koma simudziwa bwanji kuzindikira nyengo ino?
Koma Ambuye anamyankha iye, nati, Onyenga inu, kodi munthu aliyense wa inu samaimasula ng'ombe yake, kapena bulu wake ku chodyeramo, tsiku la Sabata, kupita nayo kukaimwetsa madzi?
Koma chakudya chotafuna chili cha anthu aakulu misinkhu, amene mwa kuchita nazo anazoloweretsa zizindikiritso zao kusiyanitsa chabwino ndi choipa.