Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Luka 12:56 - Buku Lopatulika

56 Onyenga inu, mudziwa kuzindikira nkhope yake ya dziko lapansi ndi ya thambo; koma simudziwa bwanji kuzindikira nyengo ino?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

56 Onyenga inu, mudziwa kuzindikira nkhope yake ya dziko lapansi ndi ya thambo; koma simudziwa bwanji kuzindikira nyengo yino?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

56 Inu anthu achiphamaso, mumatha kuzindikira maonekedwe a dziko lapansi ndi a kuthambo, koma bwanji simutha kuzindikira tanthauzo la zimene zikuchitika masiku omwe ano?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

56 Achiphamaso inu! Inu mumadziwa kutanthauzira maonekedwe a dziko lapansi ndi thambo. Zikutheka bwanji kuti simukudziwa kumasulira kwa nthawi ino?

Onani mutuwo Koperani




Luka 12:56
12 Mawu Ofanana  

Ndi a ana a Isakara, anthu akuzindikira nyengo, akudziwa zoyenera Israele kuzichita, akulu ao ndiwo mazana awiri; ndi abale ao onse anapenyerera pakamwa pao.


ndipo ndidzagwedeza amitundu onse, ndi zofunika za amitundu onse zidzafika, ndipo ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero, ati Yehova wa makamu.


Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.


Koma inu akuopa dzina langa, dzuwa la chilungamo lidzakutulukirani, muli kuchiritsa m'mapiko mwake; ndipo mudzatuluka ndi kutumphatumpha ngati anaang'ombe onenepa otuluka m'khola.


Nyengo imeneyo Yesu anayankha nati, Ndivomerezana ndi Inu, Atate, Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, kuti munazibisira izo kwa anzeru ndi akudziwitsa, ndipo munaziululira zomwe kwa makanda:


Ndipo m'mawa, Lero nkwa mphepo: popeza thambo lili la cheza chodera. Mudziwa kuzindikira za pa nkhope ya thambo; koma zizindikiro za nyengo ino, simungathe kuzindikira.


Chifukwa chake pamene paliponse upatsa mphatso zachifundo, usamaomba lipenga patsogolo pako, monga amachita onyenga m'masunagoge, ndi m'makwalala, kotero kuti atamandidwe ndi anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.


koma pokwaniridwa nthawi, Mulungu anatuma Mwana wake, wobadwa ndi mkazi, wobadwa wakumvera lamulo,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa