Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 13:15 - Buku Lopatulika

15 Koma Ambuye anamyankha iye, nati, Onyenga inu, kodi munthu aliyense wa inu samaimasula ng'ombe yake, kapena bulu wake ku chodyeramo, tsiku la Sabata, kupita nayo kukaimwetsa madzi?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Koma Ambuye anamyankha iye, nati, Onyenga inu, kodi munthu aliyense wa inu samaimasula ng'ombe yake, kapena bulu wake ku chodyeramo, tsiku la Sabata, kupita nayo kukaimwetsa madzi?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Koma Ambuye adati, “Anthu achiphamaso inu, kodi suja nonsenu mumamasula ng'ombe zanu kapena abulu anu pa tsiku la Sabata kukaŵamwetsa madzi?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Ambuye anamuyankha kuti, “Iwe wachiphamaso! Kodi nonsenu simumasula pa Sabata ngʼombe zanu kapena bulu kumuchotsa mʼkhola ndi kupita naye kukamupatsa madzi?

Onani mutuwo Koperani




Luka 13:15
16 Mawu Ofanana  

kuti munthu wonyoza Mulungu asachite ufumu, ndi anthu asakodwe mumsampha.


Wonyoza Mulungu aononga mnzake ndi m'kamwa mwake; koma olungama adzapulumuka pakudziwa.


Pakuti woopsa wagoma, ndi wonyoza watha, ndi onse odikira zolakwa alikhidwa;


Kawalekeni iwo, ali atsogoleri akhungu. Ndipo ngati wakhungu amtsogolera wakhungu, onse awiri adzagwa m'mbuna.


Onyenga inu! Yesaya ananenera bwino za inu, ndi kuti,


Koma tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pao; pakuti inu nokha simulowamo, ndipo muwaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo.


Chomwecho inunso muonekera olungama pamaso pa anthu, koma m'kati muli odzala ndi chinyengo ndi kusaweruzika.


Wonyenga iwe! Tayamba kuchotsa m'diso lako mtandawo, ndipo pomwepo udzapenyetsa kuchotsa kachitsotso m'diso la mbale wako.


Pomwepo pamene anthu a zikwizikwi a khamu anasonkhana pamodzi, kotero kuti anapondana, Iye anayamba kunena kwa ophunzira ake poyamba, Tachenjerani nokha ndi chotupitsa mikate cha Afarisi, chimene chili chinyengo.


Ndipo anati kwa iwo, Ndani wa inu bulu wake kapena ng'ombe yake itagwa m'chitsime, ndipo sadzaitulutsa pomwepo tsiku la Sabata kodi?


Kapena ungathe bwanji kunena kwa mbale wako, Mbale iwe, leka ndichotse kachitsotso kali m'diso lako, wosayang'anira iwe mwini mtanda uli m'diso lako? Wonyenga iwe! Yamba wachotsa mtandawo m'diso lako, ndipo pomwepo udzayang'anitsa bwino kuchotsa kachitsotso ka m'diso la mbale wako.


Ndipo pamene Ambuye anamuona, anagwidwa ndi chifundo chifukwa cha iye, nanena naye, Usalire.


Ndipo Yohane anaitana awiri a ophunzira ake, nawatuma kwa Ambuye, nanena, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang'anire wina?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa