Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 13:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo mkulu wa sunagoge anavutika mtima, chifukwa Yesu anachiritsa tsiku la Sabata, nayankha, nanena kwa khamulo, Alipo masiku asanu ndi limodzi, m'menemo anthu ayenera kugwira ntchito, chifukwa chake idzani kudzachiritsidwa momwemo, koma tsiku la Sabata ai.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo mkulu wa sunagoge anavutika mtima, chifukwa Yesu anachiritsa tsiku la Sabata, nayankha, nanena kwa khamulo, Alipo masiku asanu ndi limodzi, m'menemo anthu ayenera kugwira ntchito, chifukwa chake idzani kudzachiritsidwa momwemo, koma tsiku la Sabata ai.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Koma mkulu wa nyumba yamapemphero ija adakwiya, poona kuti Yesu wachiritsa munthu pa tsiku la Sabata. Tsono mkuluyo adauza anthu onse kuti, “Pali masiku asanu ndi limodzi antchito. Muzibwera masiku ameneŵa kudzachiritsidwa, osati pa tsiku la Sabata ai”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Chifukwa cha kuyipidwa kuti Yesu anachiritsa pa Sabata, wolamulira sunagoge anati kwa anthu, “Pali masiku asanu ndi limodzi ogwira ntchito. Choncho bwerani kuti mudzachiritsidwe masiku amenewo osati pa Sabata.”

Onani mutuwo Koperani




Luka 13:14
20 Mawu Ofanana  

Masiku asanu ndi limodzi uzigwira, ndi kumaliza ntchito zako zonse;


Uzichita ntchito yako masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri uzipumula; kuti ng'ombe yako ndi bulu wako zipumule, ndi kuti mwana wa mdzakazi wako ndi mlendo atsitsimuke.


Ndipo ndinawapatsanso masabata anga akhale chizindikiro pakati pa Ine ndi iwo, kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova wakuwapatula.


Popeza mukankha ndi nthiti ndi phewa, nimugunda zodwala zonse ndi nyanga zanu, mpaka mwazibalalitsa kubwalo,


Masiku asanu ndi limodzi azigwira ntchito; koma lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata lakupumula, msonkhano wopatulika; musamagwira ntchito konse; ndilo Sabata la Yehova m'nyumba zanu zonse.


Koma Afarisi, pakuona, anati kwa Iye, Tapenyani, ophunzira anu achita chosaloleka tsiku la Sabata.


Ndipo anadzako mmodzi wa akulu a sunagoge, dzina lake Yairo; ndipo pakuona Iye, anagwada pa mapazi ake, nampempha kwambiri,


Koma iwowo anagwidwa misala; nalankhulana wina ndi mnzake kuti amchitire Yesu chiyani.


Ndipo alembi ndi Afarisi analikumzonda Iye, ngati adzachiritsa tsiku la Sabata; kuti akapeze chomneneza Iye.


Ndipo onani, panadza munthu dzina lake Yairo, ndipo iye ndiye mkulu wa sunagoge; ndipo anagwa pamapazi ake a Yesu, nampempha Iye adze kunyumba kwake;


Ndipo m'mene adatha kuwerenga chilamulo ndi aneneri, akulu a sunagoge anatuma wina kwa iwo, ndi kunena, Amuna inu, abale, ngati muli nao mau akudandaulira anthu, nenani.


Ndipo anamgwira Sostene, mkulu wa sunagoge, nampanda kumpando wachiweruziro. Ndipo Galio sanasamalire zimenezi.


Ndipo Krispo, mkulu wa sunagoge, anakhulupirira Ambuye, ndi apabanja ake onse; ndipo Akorinto ambiri anamva, nakhulupirira, nabatizidwa.


Pakuti ndiwachitira iwo umboni kuti ali ndi changu cha kwa Mulungu, koma si monga mwa chidziwitso.


Masiku asanu ndi limodzi uzigwiritsa ntchito, ndi kuchita ntchito zako zonse;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa