Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 13:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo mkazi uyu, ndiye mwana wa Abrahamu, amene Satana anammanga, onani, zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu, nanga si kuyenera kodi, kuti amasulidwe nsinga yake imeneyi tsiku la Sabata?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo mkazi uyu, ndiye mwana wa Abrahamu, amene Satana anammanga, onani, zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu, nanga si kuyenera kodi, kuti amasulidwe nsinga yake imeneyi tsiku la Sabata?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Nanga maiyu, amene ali mwana wa Abrahamu, ndipo Satana adaamumanga zaka 18, kodi sikunayenera kuti amasulidwe ku nsinga imeneyi pa tsiku la Sabata?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Nanga mayiyu, amene ndi mwana wa Abrahamu, ndipo anamangidwa ndi Satana zaka 18, kodi siwoyenera kuti amasulidwe msinga imeneyi pa tsiku la Sabata?”

Onani mutuwo Koperani




Luka 13:16
11 Mawu Ofanana  

Anawatulutsa mumdima ndi mu mthunzi wa imfa, nadula zomangira zao.


Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Choka Satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzamgwadira, ndipo Iye yekhayekha udzamlambira.


Ndipo ananena nao, Sabata linaikidwa chifukwa cha munthu, si munthu chifukwa cha Sabata;


Ndipo anakweza mau nati, Atate Abrahamu, mundichitire chifundo, mutume Lazaro, kuti aviike nsonga ya chala chake m'madzi, naziziritse lilime langa; pakuti ndizunzidwadi m'lawi ili la moto.


Ndipo Yesu anati kwa iye, Lero chipulumutso chagwera nyumba iyi, popeza iyenso ndiye mwana wa Abrahamu.


Chifukwa chake balani zipatso zakuyenera kulapa mtima, ndipo musayambe kunena mwa inu nokha, Atate wathu tili naye ndiye Abrahamu: pakuti ndinena kwa inu, kuti ali ndi mphamvu Mulungu, mwa miyala iyi, kuukitsira Abrahamu ana.


Inu muli ochokera mwa atate wanu mdierekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaime m'choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza.


Amuna, abale, ana a mbadwa ya Abrahamu, ndi iwo mwa inu akuopa Mulungu, kwa ife atumidwa mau a chipulumutso ichi.


ndipo akadzipulumutse kumsampha wa mdierekezi, m'mene anagwidwa naye, kuchifuniro chake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa