Musamatero ai, kupha olungama pamodzi ndi oipa, kuta olungama akhale monga oipa; musamatero ai; kodi sadzachita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi?
Masalimo 9:8 - Buku Lopatulika Ndipo Iyeyu adzaweruza dziko lapansi m'chilungamo, nadzaweruza anthu molunjika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Iyeyu adzaweruza dziko lapansi m'chilungamo, nadzaweruza anthu molunjika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iye amaweruza dziko lapansi molungama, amagamula milandu ya anthu mosakondera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye adzaweruza dziko mwachilungamo; adzalamulira mitundu ya anthu mosakondera. |
Musamatero ai, kupha olungama pamodzi ndi oipa, kuta olungama akhale monga oipa; musamatero ai; kodi sadzachita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi?
Ndipo zakumwamba zionetsera chilungamo chake; pakuti Mulungu mwini wake ndiye woweruza.
Pakuti chiweruzo chidzabwera kunka kuchilungamo, ndipo oongoka mtima onse adzachitsata.
Pamaso pa Yehova, pakuti akudza; pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi Adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo, ndi mitundu ya anthu ndi choonadi.
Pamaso pa Yehova, popeza akudza kudzaweruza dziko lapansi; adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo, ndipo mitundu ya anthu molunjika.
Ndipo mphamvu ya mfumu ikonda chiweruzo; Inu mukhazikitsa zolunjika, muchita chiweruzo ndi chilungamo mu Yakobo.
Koma Yehova ndiye Mulungu woona; ndiye Mulungu wamoyo, mfumu yamuyaya; pa mkwiyo wake dziko lapansi lidzanthunthumira, ndi amitundu sangapirire ukali wake.
chifukwa anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m'chilungamo, ndi munthu amene anamuikiratu; napatsa anthu onse chitsimikizo, pamene anamuukitsa Iye kwa akufa.
tsiku limene Mulungu adzaweruza ndi Khristu Yesu zinsinsi za anthu, monga mwa Uthenga wanga Wabwino.