Munditsogolere m'choonadi chanu, ndipo mundiphunzitse; pakuti Inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; Inu ndikuyembekezerani tsiku lonseli.
Masalimo 86:3 - Buku Lopatulika Mundichitire chifundo, Ambuye; pakuti tsiku lonse ndiitana Inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mundichitire chifundo, Ambuye; pakuti tsiku lonse ndiitana Inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mundikomere mtima, Inu Ambuye, popeza kuti ndimalirira Inu tsiku lonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mundichitire chifundo, Inu Ambuye, pakuti ndikuyitana Inu tsiku lonse. |
Munditsogolere m'choonadi chanu, ndipo mundiphunzitse; pakuti Inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; Inu ndikuyembekezerani tsiku lonseli.
Pakufuula ine mundiyankhe, Mulungu wa chilungamo changa; pondichepera mwandikulitsira malo. Ndichitireni chifundo, imvani pemphero langa.
Mundichitire chifundo, Mulungu, pakuti anthu afuna kundimeza. Andipsinja pondithira nkhondo tsiku lonse.
Mundichitire chifundo, Mulungu, mundichitire chifundo; pakuti moyo wanga ukhulupirira Inu, ndipo ndithawira kumthunzi wa mapiko anu, kufikira zosakazazo zidzapita.
Diso langa lapuwala chifukwa cha kuzunzika kwanga: Ndimaitana Inu, Yehova, tsiku lonse; nditambalitsira manja anga kwa Inu.
Ndipo kodi Mulungu sadzachitira chilungamo osankhidwa ake akumuitana usana ndi usiku, popeza aleza nao mtima?
zaka zisanu ndi ziwiri, ndipo anali wamasiye wa kufikira zaka zake makumi asanu ndi atatu mphambu zinai, amene sankachoka ku Kachisi, wotumikira Mulungu ndi kusala kudya ndi kupemphera usiku ndi usana.
mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse,