Zipangizo zonse zagolide ndi zasiliva ndizo zikwi zisanu ndi mazana anai. Izi zonse Sezibazara anakwera nazo, pokwera andende aja kuchokera ku Babiloni kunka ku Yerusalemu.
Masalimo 85:1 - Buku Lopatulika Munachita zovomereza dziko lanu, Yehova; munabweza ukapolo wa Yakobo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Munachita zovomereza dziko lanu, Yehova; munabweza ukapolo wa Yakobo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu Chauta, mudakomera mtima dziko lanu, mudaŵakhazikanso pabwino a m'banja la Yakobe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova munakomera mtima dziko lanu; munabwezeretsa ulemerero wa Yakobo. |
Zipangizo zonse zagolide ndi zasiliva ndizo zikwi zisanu ndi mazana anai. Izi zonse Sezibazara anakwera nazo, pokwera andende aja kuchokera ku Babiloni kunka ku Yerusalemu.
Mwenzi chipulumutso cha Israele chitachokera ku Ziyoni! Pakubweretsa Yehova anthu ake a m'nsinga, pamenepo adzakondwera Yakobo, nadzasekera Israele.
Monga nswala ipuma wefuwefu kukhumba mitsinje; motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba Inu, Mulungu.
Atero Yehova: Taonani, ndidzabwezanso undende wa mahema a Yakobo, ndipo ndidzachitira chifundo zokhalamo zake, ndipo mzinda udzamangidwa pamuunda pake, ndi chinyumba chidzakhala momwe.
Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Kawirinso adzanena mau awa m'dziko la Yuda ndi m'mizinda yake, pamene ndibwezanso undende wao; Yehova akudalitse iwe, wokhalamo chilungamo, iwe phiri lopatulika.
Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Tsopano ndidzabweza undende wa Yakobo, ndi kuchitira chifundo nyumba yonse ya Israele, ndipo ndidzachitira dzina langa loyera nsanje.
Pakuti taonani, masiku awo, ndi nthawi iyo, pamene ndibwera nao andende a Yuda ndi a Yerusalemu,
pamenepo ndidzakumbukira pangano langa ndi Yakobo; ndiponso pangano langa ndi Isaki, ndiponso pangano langa ndi Abrahamu ndidzakumbukira; ndipo ndidzakumbukira dzikoli.
Chifukwa chake atero Yehova: Ndabwera kudza ku Yerusalemu ndi zachifundo; nyumba yanga idzamangidwamo, atero Yehova wa makamu, ndipo adzayesa Yerusalemu ndi chingwe.