Ndipo Davide anati kwa Solomoni mwana wake, Kunena za ine, kumtima kwanga kudati, ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba.
Masalimo 73:2 - Buku Lopatulika Koma ine, ndikadagwa; mapazi anga akadaterereka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ine, ndikadagwa; mapazi anga akadaterereka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ine ndinali pafupi kuphunthwa, mapazi anga anali pafupi kuterereka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma kunena za ine, mapazi anga anali pafupi kuterereka; ndinatsala pangʼono kugwa. |
Ndipo Davide anati kwa Solomoni mwana wake, Kunena za ine, kumtima kwanga kudati, ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba.
Koma ine ndidzapenyerera nkhope yanu m'chilungamo, ndidzakhuta mtima ndi maonekedwe anu, pamene ndidzauka.
Koma ine, pakudwala iwowa, chovala changa ndi chiguduli. Ndinazunza moyo wanga ndi kusala; ndipo pemphero langa linabwera kuchifuwa changa.
Koma ine, mwa kuchuluka kwa chifundo chanu ndidzalowa m'nyumba yanu; ndidzagwada kuyang'ana Kachisi wanu woyera ndi kuopa Inu.
Ndipo ngati kutumikira Yehova kukuipirani mudzisankhire lero amene mudzamtumikira, kapena milungu imene anaitumikira makolo anu okhala tsidya lija la mtsinje, kapena milungu ya Aamori amene mukhala m'dziko lao; koma ine, ndi a m'nyumba yanga, tidzatumikira Yehova.
Ndipo inenso, kukhale kutali ndi ine, kuchimwira Yehova ndi kuleka kukupemphererani; koma ndidzakulangizani njira yabwino ndi yolungama.
Adzasunga mapazi a okondedwa ake, koma oipawo adzawakhalitsa chete mumdima; pakuti palibe munthu adzapambana ndi mphamvu.