Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 73:3 - Buku Lopatulika

3 Pakuti ndinachitira nsanje odzitamandira, pakuona mtendere wa oipa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Pakuti ndinachitira nsanje odzitamandira, pakuona mtendere wa oipa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Pakuti ndinkachita nsanje ndi anthu odzikuza, pamene ndidaona anthu oipa akulemera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Pakuti ndinkachitira nsanje odzitamandira, pamene ndinaona mtendere wa anthu oyipa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 73:3
14 Mawu Ofanana  

Mahema a achifwamba akhala mumtendere, ndi iwo oputa Mulungu alimbika mtima; amene Mulungu amadzazira dzanja lao.


Anthu oongoka mtima adzadabwa nacho, ndi munthu wosalakwa adzadziutsa kumtsutsa wonyoza Mulunguyo.


Oipa akhaliranji ndi moyo, nakalamba, nalemera kwakukulu?


Awalola akhale osatekeseka, ndipo alimbikapo; koma maso ake ali panjira zao.


Mayendedwe ake alimbika nthawi zonse; maweruzo anu ali pamwamba posaona iye; adani ake onse awanyodola.


Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa, usachite nsanje chifukwa cha ochita chosalungama.


Khala chete mwa Yehova, numlindirire Iye; usavutike mtima chifukwa cha iye wolemerera m'njira yake, chifukwa cha munthu wakuchita chiwembu.


Mtima wako usachitire nsanje akuchimwawo; koma opabe Yehova tsiku lonse.


Usachitire nsanje anthu oipa, ngakhale kufuna kukhala nao;


Usachitire nsanje munthu wachiwawa; usasankhe njira yake iliyonse.


Ndaona zonsezi masiku anga achabe; pali wolungama angofa m'chilungamo chake, ndipo pali woipa angokhalabe ndi moyo m'kuipa kwake.


Wolungama ndinu, Yehova, pamene nditsutsana nanu mlandu; pokhapo ndinenane nanu za maweruzo; chifukwa chanji ipindula njira ya oipa? Chifukwa chanji akhala bwino onyengetsa?


Ndipo tsopano tiwatcha odzikuza odala, inde iwo ochita zoipa amangidwa ngati nyumba; inde, ayesa Mulungu, napulumuka.


Kodi muyesa kapena kuti malembo angonena chabe? Kodi Mzimuyo adamkhalitsa mwa ife akhumbitsa kuchita nsanje?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa