Masalimo 72:4 - Buku Lopatulika Adzaweruza ozunzika a mwa anthu, adzapulumutsa ana aumphawi, nadzaphwanya wosautsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Adzaweruza ozunzika a mwa anthu, adzapulumutsa ana aumphawi, nadzaphwanya wosautsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mfumu idzateteza anthu osauka, idzapulumutsa anthu osoŵa, koma idzaononga anthu ozunza anzao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye adzateteza ozunzika pakati pa anthu ndi kupulumutsa ana a anthu osowa; adzaphwanya ozunza anzawo. |
Popeza adzaima padzanja lamanja la waumphawi, kumpulumutsa kwa iwo akuweruza koipa moyo wake.
koma ndi chilungamo adzaweruza aumphawi, nadzadzudzulira ofatsa a m'dziko moongoka; ndipo adzamenya dziko lapansi ndi chibonga cha kukamwa kwake, nadzapha oipa ndi mpweya wa milomo yake.
Taona Mtumiki wanga, amene ndimgwiriziza; Wosankhika wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; ndaika mzimu wanga pa Iye; Iye adzatulutsira amitundu chiweruziro.
Bango lophwanyika sadzalithyola, ndi lawi lozilala sadzalizima; adzatulutsa chiweruzo m'zoona.
Pakuti goli la katundu wake, ndi mkunkhu wa paphewa pake, ndodo ya womsautsa, inu mwazithyola monga tsiku la Midiyani.
Ndipo linathyoka tsikulo, momwemo zonyankhalala za zoweta, zakundisamalira Ine, zinadziwa kuti ndiwo mau a Yehova.
M'mwemo ndinadyetsa zoweta zakukaphedwa, ndizo zoweta zonyankhalala. Ndipo ndinadzitengera ndodo ziwiri; ina ndinaitcha Chisomo, inzake ndinaitcha Chomanganitsa; ndipo ndinadyetsa zowetazo.
akhungu alandira kuona kwao, ndi opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ndi ogontha akumva, ndi akufa aukitsidwa, ndi kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino.
Kondwera pa iye, m'mwamba iwe, ndi oyera mtima, ndi atumwi, ndi aneneri inu; chifukwa Mulungu anauweruzira kuweruzidwa kwanu.
Ndipo momwemo munapezedwa mwazi wa aneneri ndi oyera mtima, ndi onse amene anaphedwa padziko.
pakuti maweruzo ake ali oona ndi olungama; ndipo anaweruza mkazi wachigololo wamkulu, amene anaipsa dziko ndi chigololo chake, ndipo anabwezera chilango mwazi wa akapolo ake padzanja lake la mkaziyo.