Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 11:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo linathyoka tsikulo, momwemo zonyankhalala za zoweta, zakundisamalira Ine, zinadziwa kuti ndiwo mau a Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo linathyoka tsikulo, momwemo zonyankhalala za zoweta, zakundisamalira Ine, zinadziwa kuti ndiwo mau a Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Motero chipanganocho chidatha tsiku limenelo, ndipo ochita malonda a nkhosa aja, amene ankangondiyang'anitsitsa, adazindikira kuti zonse zimene ndinkachita zinali zochokera kwa Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Linaphwanyidwa tsiku limenelo ndipo nkhosa zosautsidwa zimene zimandiyangʼanitsitsa zinadziwa kuti anali mawu a Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 11:11
27 Mawu Ofanana  

osawerenga uja anabwera naye amalonda oyendayenda, ndi amalonda ena; ndipo mafumu onse a Arabiya, ndi akazembe a dziko, anadza naye golide ndi siliva kwa Solomoni.


Pakuti Yehova amvera aumphawi, ndipo sapeputsa am'ndende ake.


Ndipo adzayankhanji amithenga a amitundu? Kuti Yehova wakhazikitsa Ziyoni, ndipo m'menemo anthu ake ovutidwa adzaona pobisalira.


koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.


Ndipo ndidzalindira Yehova, amene wabisira a nyumba ya Yakobo nkhope yake, ndipo ndidzamyembekeza Iye.


Ndipo Hanamele mwana wa mbale wa atate wanga anadza kwa ine m'bwalo la kaidi monga mwa mau a Yehova, nati kwa ine, Gulatu munda wanga, wa ku Anatoti, m'dziko la Benjamini; pakuti mphamvu yakulowa ndi yakuombola ndi yako; udzigulire wekha. Pamenepo ndinadziwa kuti awa ndi mau a Yehova.


Koma ine, ndidzadikira Yehova; ndidzalindirira Mulungu wa chipulumutso changa; Mulungu wanga adzandimvera.


Koma ndidzasiya pakati pako anthu ozunzika ndi osauka, ndipo iwo adzakhulupirira dzina la Yehova.


ndipo sanapeze chimene akachita; pakuti anthu onse anamlendewera Iye kuti amve.


Ndipo onani, mu Yerusalemu munali munthu, dzina lake Simeoni; ndipo munthu uyu, wolungama mtima ndi wopemphera, analikulindira matonthozedwe a Israele; ndipo Mzimu Woyera anali pa iye.


Ndipo iye anafikako pa nthawi yomweyo, navomerezanso kutama Mulungu, nalankhula za Iye kwa anthu onse akuyembekeza chiombolo cha Yerusalemu.


(amene sanavomereze kuweruza kwao ndi ntchito yao) wa ku Arimatea, mudzi wa Ayuda, ndiye woyembekezera Ufumu wa Mulungu,


Ndipo anayankha, nati kwa iwo, Mukani, muuze Yohane zimene mwaziona, nimwazimva; anthu akhungu alandira kuona kwao, opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ogontha akumva, akufa aukitsidwa, kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino.


Ndipo kudzakhala, zitawafikira zoipa ndi zovuta zambiri, nyimbo iyi idzachita mboni pamaso pao; popeza siidzaiwalika m'kamwa mwa mbeu zao; popeza ndidziwa zolingirira zao azichita lero lino, ndisanawalowetse m'dziko limene ndinalumbira.


Pakuti ndidziwa kuti nditamwalira ine mudzadziipsa ndithu, ndi kupatuka m'njira imene ndinakuuzani; ndipo chidzakugwerani choipa masiku otsiriza; popeza mudzachita choipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wake ndi ntchito za manja anu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa