Chivumbulutso 19:2 - Buku Lopatulika2 pakuti maweruzo ake ali oona ndi olungama; ndipo anaweruza mkazi wachigololo wamkulu, amene anaipsa dziko ndi chigololo chake, ndipo anabwezera chilango mwazi wa akapolo ake padzanja lake la mkaziyo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 pakuti maweruzo ake ali oona ndi olungama; ndipo anaweruza mkazi wachigololo wamkulu, amene anaipsa dziko ndi chigololo chake, ndipo anabwezera chilango mwazi wa akapolo ake pa dzanja lake la mkaziyo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 pakuti chiweruzo chake chilichonse nchoona ndi cholungama. Iye waweruza mkazi wadama wotchuka uja amene ankaipitsa dziko lapansi ndi chigololo chake, wamlanga chifukwa cha kupha atumiki ake.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 pakuti chiweruzo chake ndi choona ndi cha chilungamo. Iye waweruza mkazi wadama wotchuka uja amene anayipitsa dziko lonse lapansi ndi zigololo zake. Iye wabwezera pa mkaziyo magazi a atumiki ake.” Onani mutuwo |