Anakhulupirira Yehova Mulungu wa Israele; atafa iye panalibe wakunga iye mwa mafumu onse a Yuda, ngakhale mwa iwo okhalapo asanabadwe iye.
Masalimo 71:1 - Buku Lopatulika Ndikhulupirira Inu, Yehova. Ndisachite manyazi nthawi zonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndikhulupirira Inu, Yehova. Ndisachite manyazi nthawi zonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ine ndimathaŵira kwa Inu Chauta. Musandichititse manyazi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwa Inu Yehova ine ndathawiramo; musalole kuti ndichititsidwe manyazi. |
Anakhulupirira Yehova Mulungu wa Israele; atafa iye panalibe wakunga iye mwa mafumu onse a Yuda, ngakhale mwa iwo okhalapo asanabadwe iye.
Ndipo anathandizidwa polimbana nao; ndi Ahagiri anaperekedwa m'dzanja lao, ndi onse anali nao; pakuti anafuulira kwa Mulungu pomenyana nao, ndipo anapembedzeka nao, popeza anamkhulupirira Iye.
Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti amthandize, chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake.
Koma Israele adzapulumutsidwa ndi Yehova ndi chipulumutso chosatha; inu simudzakhala ndi manyazi, pena kuthedwa nzeru kunthawi zosatha.
Iwo akhale ndi manyazi amene andisautsa ine, koma ine ndisakhale ndi manyazi; aopsedwe iwo, koma ndisaopsedwe ine; muwatengere iwo tsiku la choipa, muwaononge ndi chionongeko chowirikiza.
monganso kwalembedwa, kuti, Onani, ndikhazika mu Ziyoni mwala wakukhumudwa nao, ndi thanthwe lophunthwitsa; ndipo wakukhulupirira Iye sadzachita manyazi.
Chifukwa kwalembedwa m'lembo, Taona, ndiika mu Ziyoni mwala wotsiriza wa pangodya, wosankhika, wa mtengo wake; ndipo wokhulupirira Iye sadzanyazitsidwa.