Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 22:5 - Buku Lopatulika

5 Anafuula kwa Inu, napulumutsidwa; anakhulupirira Inu, ndipo sanachite manyazi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Anafuula kwa Inu, napulumutsidwa; anakhulupirira Inu, ndipo sanachite manyazi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Ankalirira Inu, ndipo Inu munkaŵalanditsa. Ankakhulupirira Inu, ndipo Inu simunkaŵagwiritsa mwala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Analirira kwa inu ndipo munawapulumutsa. Iwo anakhulupirira Inu ndipo simunawakhumudwitse.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 22:5
17 Mawu Ofanana  

Ndipo anathandizidwa polimbana nao; ndi Ahagiri anaperekedwa m'dzanja lao, ndi onse anali nao; pakuti anafuulira kwa Mulungu pomenyana nao, ndipo anapembedzeka nao, popeza anamkhulupirira Iye.


Koma anapenya nsautso yao, pakumva kufuula kwao:


Ndakhulupirira Inu, Yehova, ndikhale wopanda manyazi nthawi zonse, mwa chilungamo chanu ndipulumutseni ine.


Ndikhulupirira Inu, Yehova. Ndisachite manyazi nthawi zonse.


Koma Israele adzapulumutsidwa ndi Yehova ndi chipulumutso chosatha; inu simudzakhala ndi manyazi, pena kuthedwa nzeru kunthawi zosatha.


Ndipo mafumu adzakulera, ndi akazi ao aakulu adzakuyamwitsa; iwo adzakugwadira ndi nkhope zao zoyang'ana pansi, nadzaseteka fumbi la m'mapazi ako: ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndi iwo amene alindira Ine sadzakhala ndi manyazi.


Onse amene anazipeza anazidya; adani ao anati, Sitipalamula mlandu, chifukwa iwo anachimwira Yehova, ndiye mokhalamo zolungama, Yehova, chiyembekezo cha atate ao.


Nebukadinezara ananena, nati, Alemekezedwe Mulungu wa Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, amene anatuma mthenga wake, napulumutsa atumiki ake omkhulupirira Iye, nasanduliza mau a ine mfumu, napereka matupi ao kuti asatumikire kapena kulambira mulungu wina yense, koma Mulungu waowao.


Pakuti lembo litere, Amene aliyense akhulupirira Iye, sadzachita manyazi.


monganso kwalembedwa, kuti, Onani, ndikhazika mu Ziyoni mwala wakukhumudwa nao, ndi thanthwe lophunthwitsa; ndipo wakukhulupirira Iye sadzachita manyazi.


Chifukwa kwalembedwa m'lembo, Taona, ndiika mu Ziyoni mwala wotsiriza wa pangodya, wosankhika, wa mtengo wake; ndipo wokhulupirira Iye sadzanyazitsidwa.


Ndipo ana a Israele anafuula kwa Yehova; pakuti anali nao magaleta achitsulo mazana asanu ndi anai; napsinja ana a Israele kolimba zaka makumi awiri.


Ndipo Israele anafooka kwambiri chifukwa cha Midiyani; ndipo ana a Israele anafuula kwa Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa